bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Song of Solomon 7
Song of Solomon 7
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 8 →
1
Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata, mwana wamkaziwe wa mfumu! Pozinga m'chuuno mwako pakunga zonyezimira, ntchito ya manja a mmisiri waluso.
2
Pamchombo pako pakunga chikho choulungika, chosasowamo vinyo wosanganika: Pamimba pako pakunga mulu wa tirigu wozingidwa ndi akakombo.
3
Mawere ako akunga ana awiri a nswala anabadwa limodzi.
4
Khosi lako likunga nsanja yaminyanga; maso ako akunga matawale a ku Hesiboni, a pa chipata cha Batirabimu; mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebanoni imene iloza ku Damasiko.
5
Mutu wako ukunga Karimele, ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsalu yofiirira; mfumu yamangidwa ndi nkhata zake ngati wam'nsinga.
6
Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika, bwenziwe, m'zokondweretsa!
7
Msinkhu wakowu ukunga mgwalangwa, mawere ako akunga matsango amphesa.
8
Ndinati, Ndikakwera pa mgwalangwapo, ndikagwira nthambi zake: Mawere ako ange ngati matsango amphesa, ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula.
9
M'kamwa mwako munge ngati vinyo woposa, womeza tseketseke bwenzi langa, wolankhulitsa milomo ya ogona tulo.
10
Ndine wa wokondedwa wanga mnyamatayo, ndine amene andifunayo.
11
Tiye, bwenzi langa, tinke kuminda; titsotse m'milaga.
12
Tilawire kunka kuminda yamipesa; tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso, makangaza ndi kutuwa maluwa ake; pompo ndidzakupatsa chikondi changa.
13
Mankhwala a chikondi anunkhira, ndi pamakomo pathu zipatso zabwino, za mitundumitundu, zakale ndi zatsopano, zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8