bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Song of Solomon 5
Song of Solomon 5
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 6 →
1
Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi: Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga; ndadya uchi wanga ndi chisa chake; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi.
2
Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso: Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati, nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga, nkhunda yanga, wangwiro wanga: Pakuti pamtu panga padzala mame, patsitsi panga pali madontho a usiku.
3
Ndinayankha kuti, Ndavula malaya anga, ndiwavalenso bwanji? Ndasuka mapazi anga; ndiwadetserenji?
4
Bwenzi langa analonga dzanja lake pazenera, mtima wanga ndi kuguguda chifukwa cha iye.
5
Ndinauka ndikatsegulire bwenzi langa; pamanja panga panakha mure. Ndi pa zala zanga madzi a mure, pa zogwirira za mpikizo.
6
Ndinamtsegulira bwenzi langalo; koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka. Moyo wanga unalefuka polankhula iye: Ndinamfunafuna, osampeza; ndinamuitana, koma sanandivomere.
7
Alonda akuyenda m'mudzi anandipeza, nandikantha, nanditema; osunga makoma nandichotsera chophimba changa.
8
Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani? Kuti ndadwala ndi chikondi.
9
Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji, mkaziwe woposa kukongola? Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji, kuti utilumbirira motero?
10
Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira, womveka mwa zikwi khumi.
11
Mutu wake ukunga golide, woyengetsa, tsitsi lake lopotana, ndi lakuda ngati khungubwi.
12
Ana a maso ake akunga nkhunda pambali pa mitsinje ya madzi; otsukidwa ndi mkaka, okhala pa mitsinje yodzala.
13
Masaya ake akunga chitipula chobzalamo ndiwo, ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira: Milomo yake ikunga akakombo, pakukhapo madzi a mure.
14
Manja ake akunga zing'anda zagolide zoikamo zonyezimira zoti biriwiri. Thupi lake likunga chopanga cha minyanga cholemberapo masafiro.
15
Miyendo yake ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira, zogwirika m'kamwa mwa golide: Maonekedwe ake akunga Lebanoni, okometsetsa ngati mikungudza.
16
M'kamwa mwake muli mokoma; inde, ndiye wokondweretsa ndithu. Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa, ana akazi inu a ku Yerusalemu.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8