bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Song of Solomon 6
Song of Solomon 6
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 7 →
1
Bwenzi lako wapita kuti, mkaziwe woposa kukongola? Bwenzi lako wapatukira kuti, tikamfunefune pamodzi nawe?
2
Bwenzi langa watsikira kumunda kwake, kuzitipula za mphoka, kukadya kumunda kwake, ndi kutchera akakombo.
3
Ndine wake wa wokondedwa wanga, wokondedwa wanganso ndiye wa ine; aweta zake pakati pa akakombo.
4
Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza, wokoma ngati Yerusalemu, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera.
5
Undipambutsire maso ako, pakuti andiopetsa. Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi, zigona pambali pa Giliyadi.
6
Mano ako akunga gulu la nkhosa zazikazi, zikwera kuchokera kosamba; yonse ili ndi ana awiri, palibe imodzi yopoloza.
7
Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseli pa chophimba chako.
8
Alipo akazi akulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi, kudza akazi aang'ono makumi asanu ndi atatu, ndi anamwali osawerengeka.
9
Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi; ndiye wobadwa yekha wa amake; ndiye wosankhika wa wombala. Ana akazi anamuona, namutcha wodala; ngakhale akazi akulu a mfumu, ndi akazi aang'ono namtamanda.
10
Nati, Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha, wokongola ngati mwezi, woyera ngati dzuwa, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera?
11
Ndinatsikira kumunda wa mtedza, kukapenya msipu wa m'chigwa, kukapenya ngati pamipesa paphuka, ngati pamakangaza patuwa maluwa.
12
Ndisanazindikire, moyo wanga unandiimika pakati pa magaleta a anthu anga aufulu.
13
Anati, Bwera, bwera, Msulamiwe; bwera, bwera, tiyang'ane pa iwe. Muyang'aniranji pa Msulami, ngati pa masewero akuguba?
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8