bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Song of Solomon 3
Song of Solomon 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 4 →
1
Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda: Ndinamfunafuna, koma osampeza.
2
Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m'mudzi, m'makwalala ndi m'mabwalo ake, ndimfunefune amene moyo wanga umkonda: Ndimfunafuna, koma osampeza.
3
Alonda akuyendayenda m'mudzi anandipeza: Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?
4
Nditawapitirira pang'ono, ndinampeza amene moyo wanga umkonda: Ndinamgwiriziza, osamfumbatula, mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai, ngakhale m'chipinda cha wondibala.
5
Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala ya kuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini.
6
Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo, wonunkhira ndi mure ndi lubani, ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?
7
Taonani, ndi machila a Solomoni; pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi, a mwa ngwazi za Israele.
8
Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo: Yense ali ndi lupanga lake pantchafu pake, chifukwa cha upandu wa usiku.
9
Solomoni mfumu anadzipangira machila okhalamo tsonga ndi matabwa a ku Lebanoni.
10
Anapanga timilongoti take ndi siliva, cha pansi pake ndi golide, mpando wake ndi nsalu yofiirira, pakati pake panayalidwa za chikondi cha ana akazi a ku Yerusalemu.
11
Tulukani, ana akazi inu a Ziyoni, mupenye Solomoni mfumu, ndi korona amake amamveka naye tsiku la ukwati wake, ngakhale tsiku lakukondwera mtima wake.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8