bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Romans 14
Romans 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 15 →
1
Mlandireni bwino munthu amene chikhulupiriro chake nchofooka, koma osati kuti mutsutsane naye pa maganizo ake.
2
Wina amakhulupirira kuti palibe choletsa kudya chakudya chilichonse. Koma wina, amene chikhulupiriro chake nchofooka, amadya zamasamba zokha.
3
Amene amadya chilichonse, asanyoze mnzake amene amazisala. Amene amasala zinthu zina asaweruze mnzake amene amazidya, pakuti Mulungu wamulandira.
4
Kodi iweyo ndiwe yani kuti uweruze wantchito wamwini kuti walakwa? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza, popeza kuti Ambuye angathe kumkhozetsa.
5
Ena amaganiza kuti tsiku lakutilakuti ndi loposa masiku ena, koma pamene ena akuganiza kuti masiku onse nchimodzimodzi. Aliyense achite monga momwe watsimikizira kwenikweni mumtima mwake.
6
Amene amasunga tsiku lakutilakuti, amatero kuti alemekeze Ambuye. Amene amadya chilichonse, amatero kuti alemekeze Ambuye, pakuti amayamika Mulungu chifukwa cha chakudyacho. Amene amasala zina, amatero kuti alemekeze Ambuye, ndipo amayamika Mulungu pakutero.
7
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene amakhala moyo chifukwa cha iye yekha, kapena kufa chifukwa cha iye yekha.
8
Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
9
Paja Khristu adamwalira nakhalanso ndi moyo, kuti akhale Mbuye wa anthu akufa ndiponso wa anthu amoyo.
10
Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze.
11
Paja Malembo akunena kuti, “Ambuye akuti, ‘Pali Ine ndemwe, anthu onse adzandigwadira ndi kuvomereza kuti ndine Mulungu.’ ”
12
Motero aliyense mwa ife adzadzifotokozera yekha kwa Mulungu zimene adazichita.
13
Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa.
14
Pogwirizana ndi maganizo a Ambuye Yesu, ndikutsimikiza mosakayika konse kuti palibe chinthu chingadetse munthu pamaso pa Mulungu chifukwa wachikhudza. Koma ngati wina aganiza kuti chinthu nchomudetsa, kwa iyeyo chinthucho nchomudetsadi.
15
Ngati ukhumudwitsa mbale wako pakudya chakudya cha mtundu wakutiwakuti, ndiye kuti sukuyendanso m'chikondi. Usamuwononge ndi chakudya chako munthu amene Khristu adamufera.
16
Tsono musalole kuti anthu ena aziyese zoipa zinthu zimene inu mumaziwona kuti nzabwino.
17
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
18
Aliyense wotumikira Khristu motere, amakondweretsa Mulungu, ndipo amakhala wovomerezeka kwa anthu.
19
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
20
Chakudya chisakuwonongetseni ntchito ya Mulungu. Zakudya zonse nzololedwa kuzidya, koma nkulakwa kudya chinthu chimene chingachimwitse anzathu.
21
Nkwabwino kusadya nyama, kusamwa vinyo, ndiponso kusachita kanthu kalikonse kamene kangachimwitse mbale wako.
22
Zimene iwe umakhulupirira pa zimenezi, zikhale pakati pa iweyo ndi Mulungu. Ngwodala amene mtima wake sumutsutsa pamene atsimikiza kuchita zakutizakuti.
23
Koma munthu akamadya ali wokayika, waweruzidwa kale kuti ngwolakwa, popeza kuti zimene akuchita nzosagwirizana ndi zimene iye amakhulupirira kuti nzoyenera. Paja chilichonse chimene munthu achita, chotsutsana ndi zimene iye amakhulupirira, chimenecho ndi tchimo.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
Recommended Reading
Commentary
Romans Commentaries
→
Devotional
Romans Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→