bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Romans 4
Romans 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
1
Tsono tinene chiyani za Abrahamu, kholo la ife Ayuda? Iyeyu adapezana ndi zotani?
2
Chifukwa iye uja achipezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito zake, bwenzi atakhala nacho chifukwa chonyadira. Koma ai, pamaso pa Mulungu sangathe kunyada.
3
Paja Malembo akuti bwanji? Akuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo pakukhulupirirapo, Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.”
4
Munthu akagwira ntchito, amalandira malipiro. Malipirowo sitinena kuti ndi mphatso ai, koma timati ndi zimene munthu ayeneradi kulandira chifukwa cha ntchito zake.
5
Koma munthu atangokhulupirira, m'malo mwa kudalira ntchito zake, Mulungu amene amaŵaona kuti ngosapalamula anthu ochimwa, munthu ameneyo pakukhulupirira, Mulungu adzamuwona kuti ngwolungama pamaso pake.
6
Davide adaanenanso zomwezo pamene adati ngwodala munthu amene Mulungu amuwona kuti ngwolungama popanda ntchito. Paja iye adanena kuti,
7
“Ngodala anthu amene Mulungu adaŵakhululukira machimo ao, amene Iye adaŵafafanizira machimo ao.
8
Ngwodala munthu amene Ambuye saŵerengeranso machimo ake.”
9
Kodi madalitso ameneŵa amakhalira oumbalidwa okha, kapena ndi osaumbalidwa omwe? Amakhalira ndi osaumbalidwa omwe, popeza kuti paja Malembo tatchulaŵa akunena kuti, “Abrahamu adaakhulupirira Mulungu, tsono pakukhulupirirapo adapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.”
10
Nanga ndi liti zidachitika zimenezi? Kodi ndipo ataumbalidwa kapena asanaumbalidwe? Sizidachitike ataumbalidwa ai, koma asanaumbalidwe.
11
Kuumbalidwako kudachitika pambuyo pake, kuti chikhale ngati chizindikiro chotsimikiza kuti asanaumbalidwe, adaapezeka kale kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakukhululirira. Motero Abrahamu ndi kholo la onse okhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu amaŵaona kuti ngolungama, ngakhale ndi osaumbalidwa.
12
Ndiponso ndi kholo la onse oumbalidwa, osati okhawo amene adangoumbalidwa m'thupi mokha, komanso amene akutsata chitsanzo cha chikhulupiriro cha kholo lathu Abrahamu asanaumbalidwe.
13
Abrahamu ndi zidzukulu zake adalandira kwa Mulungu lonjezo lakuti dziko lapansi lidzakhala lao. Adalandira lonjezolo osati chifukwa cha kusunga Malamulo, koma chifukwa cha chilungamo chofumira m'chikhulupiriro.
14
Ngati ndi odalira Malamulo okha amene adzalandire zimene Mulungu adalonjeza, ndiye kuti chikhulupiriro nchopanda pake, ndipo lonjezo lija lilibe phindu.
15
Malamulo amangodzetsa chilango, koma kumene kulibe malamulo, kulibenso kuŵaphwanya.
16
Nchifukwa chake lonjezolo maziko ake ndi chikhulupiriro, kuti likhale mphatso yaulere ya Mulungu, ndipo patsimikizike kuti lonjezolo adzalilandiradi anthu ofumira kwa Abrahamu. Osati okhawo amene amasunga Malamulo a Mose ai, komanso onse okhala ndi chikhulupiriro chonga cha Abrahamu. Iye ndiyedi kholo la ife tonse.
17
Paja Malembo akuti, “Ndakuika kuti ukhale kholo la mitundu yambiri ya anthu.” Lonjezo limeneli Abrahamu adalilandira kwa Mulungu mwini amene iye ankamukhulupirira. Ndi Mulungu amene amabwezera moyo kwa akufa, ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo.
18
Mulungu adati, “Zidzukulu zako zidzachulukadi.” Ndipo ngakhale zimenezi zinali zosayembekezeka konse, Abrahamu adalimbikirabe kukhulupirira kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
19
Zaka zake zinali pafupi makumi khumi, ndipo adaadziŵa kuti thupi lake linali ngati lakufa kale, ndiponso kuti Sara anali wouma.
20
Sadaŵakayikire konse mau a Mulunguyo, koma adalimbikira m'chikhulupiriro, nayamika Mulungu.
21
Adakhulupirira ndithu kuti Mulungu angathe kuchita zimene adalonjeza.
22
Nchifukwa chake, monga mau a Mulungu akunena, “Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.”
23
Mau a m'Malemboŵa onena kuti, “Mulungu adamuwona kuti ngwolungama,” sangonena za iye yekha ai.
24
Akunenanso za ife amene tidzapezeka kuti ndife olungama pakukhulupirira Mulungu, amene adaukitsa Yesu Ambuye athu kwa akufa.
25
Yesuyo adaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha zochimwa zathu, ndipo adauka kwa akufa kuti tipezeke olungama pamaso pa Mulungu.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16