bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Romans 6
Romans 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 7 →
1
Tsono tinene chiyani? Kodi tinganene kuti tizingokhalabe mu uchimo kuti kukoma mtima kwa Mulungu kuchuluke?
2
Iyai, mpang'ono pomwe. Tidachita ngati kufa nkulekana ndi uchimo. Nanga tingakhalebe mu uchimowo bwanji?
3
Kodi inu simukudziŵa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi ubatizo womwewo tidasandukanso amodzi ndi Iye mu imfa yake?
4
Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.
5
Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pa kuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo.
6
Tidziŵa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo.
7
Pakuti munthu akafa, ndiye kuti wamasuka ku mphamvu ya uchimo.
8
Tsono ngati tidafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye.
9
Tikudziŵa kuti Khristu adauka kwa akufa, ndipo sadzafanso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye.
10
Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu.
11
Momwemonso inuyo mudziwone ochita ngati kufa nkulekana ndi uchimo, koma okhala ndi moyo wotumikira Mulungu, mogwirizana ndi Khristu.
12
Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake.
13
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
14
Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu.
15
Bwanji tsono? Kodi tizichimwabe popeza kuti chimene chimalamulira moyo wathu si Malamulo, koma kukoma mtima kwa Mulungu? Iyai, mpang'ono pomwe.
16
Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.
17
Tiyamike Mulungu! Inu kale munali akapolo a uchimo, koma tsopano mukumvera ndi mtima wonse zoona za chiphunzitso chimene mudalandira.
18
Mudamasulidwa ku uchimo, ndipo tsopano mwasanduka atumiki a Mulungu ochita zachilungamo.
19
Ndikukupherani fanizo la ukapololi kuti mungalephere kumvetsa bwino zimenezi. Kale munkadzipereka kuti mukhale akapolo a zonyansa ndi zosalongosoka zonkirankira. Chonchonso tsopano mudzipereke kuti musanduke atumiki a Mulungu ochita zachilungamo, kuti mukhale oyera mtima.
20
Pamene munali akapolo a uchimo, simunkalabadirako za zimene Mulungu amati nzolungama.
21
Nanga pamenepo mudapindula chiyani pakuchita zinthu zimene tsopano mukuchita nazo manyazi? Pajatu zimene zija mathero ake ndi imfa.
22
Koma tsopano mwamasulidwa ku uchimo, ndipo ndinu otumikira Mulungu. Phindu lake ndi kuyera mtima, ndipo potsiriza pake kulandira moyo wosatha.
23
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16