bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Romans 15
Romans 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 16 →
1
Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha.
2
Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.
3
Pakuti Khristunso sankachita zinthu kungofuna kudzikondweretsa, koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Chipongwe cha anthu okunyozani Inu chidafika pa Ine.”
4
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
5
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
6
akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
7
Tsono muzilandirana monga momwe Khristu adakulandirirani inu, kuti Mulungu alemekezedwe.
8
Chifukwa kunena zoona, Khristu adasanduka mtumiki wa Ayuda, kutsimikiza kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Adatsimikiza kukhulupirikako pakuchita zimene Mulungu adaŵalonjeza makolo ao akale aja,
9
ndiponso pakupatsa anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Nchifukwa chake ndidzakuyamikani pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
10
Akutinso, “Inu anthu a mitundu ina, kondwani pamodzi ndi anthu ake a Mulungu.”
11
Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.”
12
Nayenso mneneri Yesaya akuti, “Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera. Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.”
13
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
14
Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana.
15
Komabe m'kalata ino zina ndakulemberani mopanda mantha konse, kuti ndikukumbutseni zimenezo. Ndalemba motere popeza kuti Mulungu adandikomera mtima
16
pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera.
17
Tsono pokhala ndine wake wa Khristu Yesu, ndikunyadira ntchito imene ndikugwirira Mulungu.
18
Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga,
19
ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko.
20
Masiku onse ndinkayesetsa kulalika Uthenga Wabwino kumalo kokhako kumene dzina la Khristu linali lisanamvekebe. Ndinkaopa kumanga pa maziko amene munthu wina adaika.
21
Paja Malembo akuti “Anthu amene sadauzidwe za Iye, adzaona, amene sadamve za Iye, adzamvetsa.”
22
Pa chifukwa chimenechi ndidalephera kaŵirikaŵiri kufika kwanuko.
23
Zaka zambiri ndakhala ndikulakalaka kuti ndifike kumeneko. Ndipo tsopano, popeza kuti ndatsiriza ntchito yanga ku mbali zakuno,
24
ndikuyembekeza kudzakuwonani pamene ndidzadzera kwanuko popita ku Spaniya. Ndidzakondwera kukuchezerani masiku angapo, ndipo pambuyo pake ndifuna kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga.
25
Koma tsopanoli ndikupita ku Yerusalemu kukapereka chithandizo kwa anthu a Mulungu kumeneko.
26
Pakuti mipingo ya ku Masedoniya, ndi ya ku Akaiya idakoma mtima mpaka kupereka zothandiza osauka pakati pa anthu a Mulungu a ku Yerusalemu.
27
Inde unali ufulu kuchita zimenezi, komanso unali udindo wao kuthandiza osaukawo. Ayuda adagaŵana madalitso ao achikhristu ndi anthu a mitundu ina, choncho iwowo ayeneranso kuthandiza Ayudawo pa zosoŵa zao za moyo wathupi.
28
Tsono nditatsiriza ntchito yangayi, ndi kutula bwino lomwe kwa iwo zoperekazi, ndidzadzera kwanuko popita ku Spaniya.
29
Ndikudziŵa kuti ndikadzabwera kumeneko, ndidzabwera ndi madalitso ochuluka a Khristu.
30
Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu.
31
Mundipempherere kuti Mulungu anditchinjirize, ndisagwe m'manja mwa anthu osakhulupirira am'Yudeya. Mupempherenso kuti anthu a Mulungu a ku Yerusalemu azilandire ndi manja aŵiri zoperekazi zimene ndatumidwa kuti ndikaŵapatse.
32
Choncho, Mulungu akalola, ndidzafika kwanuko ndili wokondwa, ndipo ndidzasanguluka pocheza nanu.
33
Mulungu amene amapatsa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16