bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Romans 7
Romans 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 8 →
1
Abale, ndikulankhulatu ndi inu amene mumadziŵa za malamulo. Mukudziŵa bwino kuti malamulo amamkhudza munthu pokhapokha pamene munthuyo ali moyo.
2
Mwachitsanzo, malamulo amati mkazi wokwatiwa ngwomangidwa kwa mwamuna wake, nthaŵi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi uja amamasuka ku malamulo okhudza za mwamuna wake aja.
3
Nchifukwa chake ngati adzipereka kwa mwamuna wina, pamene mwamuna wake ali moyo, mkaziyo amati ngwachigololo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi uja wamasuka ku malamulo a ukwati, kotero kuti sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
4
Chimodzimodzi inunso, abale anga. Mudachita ngati kufa ndi kulekana ndi Malamulo popeza kuti ndinu ziwalo za thupi la Khristu. Motero tsopano ndinu a wina wake, ndiye kuti a Iye amene adauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu zipatso.
5
Pamene tinkatsata mkhalidwe wathu wachibadwa, zilakolako zoipa zimene Malamulo adaaziwutsa zinkagwira ntchito mwa ife, ndipo zidabala imfa.
6
Koma tsopano tamasuka ku Malamulowo. Tidachita ngati kufa nkulekana ndi Malamulo amene kale ankatimanga. Tsopano Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mwa njira yatsopano, osatinso mwa njira yakale ija yakungotsata Malamulo olembedwa.
7
Tsono tinene chiyani? Kodi tinene kuti Malamulo ndi auchimo? Mpang'ono pomwe. Koma Malamulowo ndiwo adandizindikiritsa za uchimo. Pakuti sindikadadziŵa kuipa kwa kusirira, Malamulo akadapanda kunena kuti, “Usasirire”.
8
Chifukwa cha lamuloli, uchimo udapeza mpata woutsa mwa ine khalidwe la masiriro osiyanasiyana. Pakuti ngati palibe malamulo, uchimo sungachite kanthu.
9
Ine kale ndinali ndi moyo opanda malamulo. Koma pamene ndidayamba kudziŵa malamulo, pomwepo uchimo udayamba kulimba,
10
ndipo ine ndidakhala ngati ndafa. Tsono malamulo omwewo amene adaayenera kufikitsa anthu ku moyo, ine adandifikitsa ku imfa.
11
Pakuti uchimo udapeza mpata chifukwa cha malamulo, ndipo mwa malamulowo udandinyenga ndi kundipha.
12
Mosakayika konse, Malamulo a Mose ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo lamulo lililonse mwa Malamulowo ndi loyera, lolungama ndi labwino.
13
Kodi tsono ndiye kuti chinthu chabwinochi chidandiphetsa? Mpang'ono pomwe. Koma uchimo ndiwo udandipha pakugwiritsa ntchito chinthu chabwinocho kuti khalidwe lenileni la uchimowo liwonekere poyera kuti ndi uchimodi. Motero kudzera mwa malamulo, uchimo umaoneka woipa kopitirira.
14
Tikudziŵa kuti Malamulo a Mose ndi opatsidwa ndi Mulungu. Koma ine ndine munthu wofooka chabe, wogulitsidwa ngati kapolo ku uchimo.
15
Sindimvetsa bwino zimene ndimachita. Pakuti sindichita zimene ndifuna kuchita, koma zomwe ndimadana nazo, nzimene ine ndimazichita.
16
Koma ngati sindifuna kuchita zoipa zimene ndimachita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti Malamulo aja ndi abwino.
17
Motero zimene zimachitikazo, sindine amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine.
18
Ndikudziŵa kuti mwa ine simukhala kanthu kabwino. Ndikamati, “ine”, ndikunena khalidwe langa lokonda zoipa. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, komabe sindizichita.
19
Sindichita zabwino zimene ndifuna, koma ndimachita zoipa zimene sindifuna.
20
Ngati ndichita zimene sindizifuna, sindinenso amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine.
21
Motero ndimaona kuti chimene chimachitika nchakuti pamene ndifuna kuchita zabwino, zoipa zili nane pomwepo.
22
Mtima wanga umakondwa ndi Malamulo a Mulungu,
23
koma m'kati mwanga ndimaona lamulo lina lolimbana ndi lamulo limene mtima wanga wavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa kapolo wa lamulo la uchimo lokhala m'kati mwanga.
24
Kalanga ine! Ndani adzandipulumutsa ku khalidwe langa lino londidzetsera imfa?
25
Tiyamike Mulungu! Adzandipulumutsa ndiye kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Motero ineyo, ndi mtima wanga ndimatumikira Malamulo a Mulungu, chonsecho ndi khalidwe langa lokonda zoipa, ndimatumikira lamulo la uchimo.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16