bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Romans 16
Romans 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
1
Ndikupereka m'manja mwanu Febe, mlongo wathu, amene ali mtumiki wa mpingo wa ku Kenkrea.
2
Mlandireni m'dzina la Ambuye, monga momwe anthu a Mulungu ayenera kulandirirana. Mumthandize monga momwe angasoŵere chithandizo chanu, pakuti iyeyo adathandiza anthu ambiri, ine ndemwenso adandithandizako.
3
Mundiperekere moni kwa Prisika ndi Akwila, anzanga otumikira Khristu Yesu.
4
Iwoŵa anali okonzeka kuphedwa kuti apulumutse moyo wanga. Si ndine ndekhatu ndikuŵathokoza, komanso mipingo yonse ya ku maiko a anthu a mitundu ina.
5
Mundiperekerenso moni kwa anthu amene amasonkhana ngati ampingo m'nyumba mwao. Moni kwa Epeneto, bwenzi langa lapamtima, amene ndi woyamba mu Asiya kukhulupirira Khristu.
6
Moni kwa Maria, amene wakhala akukugwirirani ntchito kolimba.
7
Moni kwa Androniko ndi Yunia, Ayuda anzanga amene anali nane m'ndende. Iwoŵa ndi otchuka pakati pa atumwi, ndipo ndi ine ndi iwowo adayambira ndiwo kukhala akhristu.
8
Moni kwa Ampiliato, bwenzi langa lokondedwa mwa Ambuye.
9
Moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu pa ntchito ya Khristu, ndiponso kwa Stakisi, amene ndimamkonda.
10
Moni kwa Apelesi, mkhristu wolimba uja. Moni kwa a m'banja la Aristobulo.
11
Moni kwa Herodiono, Myuda mnzanga. Moni kwa akhristu a m'banja la Narkiso.
12
Moni kwa Trifena ndi Trifosa, amene amagwira mwamphamvu ntchito ya Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwa uja, amene wachita zambiri pogwirira Ambuye ntchito.
13
Moni kwa Rufu, wotchuka pa ntchito ya Ambuye. Moninso kwa mai wake amene ali ngati mai wanganso.
14
Moni kwa Asinkrito, Filegoni, Heremesi, Patrobasi, Herimasi ndi abale onse amene ali nawo pamodzi.
15
Moni kwa Filologo ndi Juliya, kwa Nereo ndi mlongo wake, kwa Olimpasi ndi kwa anthu onse a Mulungu amene ali nawo pamodzi.
16
Mupatsane moni mwa chikondi choona. Mipingo yonse yachikhristu ikukupatsani moni.
17
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa,
18
pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
19
Anthu onse adaimva mbiri ya kumvera kwanu. Tsono ine ndikunyadira inuyo, koma ndifuna kuti mukhale anzeru pa zabwino, ndi othaŵa zoipa.
20
Ndipo Mulungu amene amapatsa mtendere, posachedwa adzatswanya Satana pansi pa mapazi anu. Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni.
21
Timoteo, mnzanga wogwira naye ntchito, akukupatsani moni. Lusio, Yasoni ndi Sosipatere, Ayuda anzanga, nawonso akuti moni.
22
Ine Tersio, mlembi chabe wa kalatayi, ndikuti moni, inu abale mwa Ambuye.
23
Akukupatsani moni Gayo, amene akundisamala ine pamodzi ndi mpingo wonse kunyumba kwake. Akukupatsani moni Erasito, msungachuma wa mzinda wonse, ndiponso Kwarto, mbale wathu. [
24
Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni nonse. Amen.]
25
Tiyeni tilemekeze Mulungu! Iye ali ndi mphamvu za kukulimbitsani potsata Uthenga Wabwino umene ndimaulalika, umene ndi mau olengeza za Yesu Khristu. Zimenezi zinali zachinsinsi, ndipo zidaabisika pa zaka zonse kuyambira kalekale.
26
Koma tsopano zatulukira poyera kudzera m'zimene aneneri adalemba, ndiponso kudzera m'lamulo la Mulungu wachikhalire zadziŵika kwa anthu a mitundu yonse, kuti azizikhulupirira ndi kuzimvera.
27
Kwa Mulungu, amene ndiye yekha wanzeru, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu mpaka muyaya. Amen.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
Recommended Reading
Commentary
Romans Commentaries
→
Devotional
Romans Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→