bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Micah 1
Micah 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 2 →
1
Pa nthaŵi ya ufumu wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda, Chauta adampatsa mthenga Mika wa ku Moreseti. Nazi zimene iyeyu adaona m'masomphenya zokhudza Samariya ndi Yerusalemu.
2
Imvani nonsenu anthu a mitundu yonse. Tchera khutu iwe dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Ambuye Chauta akuimbani mlandu, akulankhulira ku Nyumba yao yoyera.
3
Taonani, Chauta akubwera kuchokera ku malo ake. Akutsika pansi ndipo akuyenda pa nsonga za mapiri.
4
Mapiriwo akusungunuka ngati phula pa moto. Akuyenderera m'zigwa ngati madzi ochokera m'phiri.
5
Zonsezi zikuchitika chifukwa cha zoipa za zidzukulu za Yakobe, chifukwa cha machimo a banja la Israele. Ndani adachimwitsa Aisraele? Si a ku Samariya kodi? Ndani adalakwitsa Ayuda? Si a ku Yerusalemu kodi?
6
Tsono Chauta akuti, “Samariyayo ndidzamsandutsa bwinja, malo olimamo munda wamphesa. Miyala yake ndidzaitaya ku zigwa, ndipo maziko ake ndidzaŵafukula.
7
Mafano ake onse ndidzaŵaphwanyaphwanya, ndipo mitulo yake yonse idzatenthedwa m'moto. Zithunzi zonse za milungu yake ndidzaziwononga. Mphatso zake adazilandira kuchokera ku malipiro a akazi adama, choncho enanso adzazigwiritsa ntchito ngati malipiro a akazi adama.”
8
Tsono Mika adati, “Nchifukwa chake ndidzalira komvetsa chisoni. Ndidzayenda maliseche, ndidzakuwa ngati nkhandwe ndi kulira ngati nthiŵatiŵa.
9
Samariya, zilonda za uchimo wake sizingathe kupola, zafika mpaka ku Yuda. Chiwonongeko chili pafupi ndi mzinda wa anthu anga, chafika mpaka ku Yerusalemu kwenikweni.”
10
Musaŵauze zimenezi a ku Gati, musalire konse. Muvimvinizike m'fumbi ku Beteleafura, kuwonetsa chisoni.
11
Inu anthu a ku Safiri mudzapita ku ukapolo muli maliseche ndi amanyazi. Anthu a ku Zanani satuluka mu mzinda wao. Mukamva anthu a ku Betezele akulira, mudzadziŵa kuti sangathe kukuthandizani.
12
Anthu a ku Maroti ali ndi nkhaŵa poyembekeza thandizo, chifukwa Chauta wadzetsa chiwonongeko pafupi ndi Yerusalemu.
13
Mangani akavalo ku magaleta, inu anthu a ku Lakisi. Mudatsanzira machimo a Israele, potero mudachimwitsa anthu a ku Ziyoni.
14
Tsono a ku Moreseti-Gati mutsazikane nawo. Anthu a ku Akizibu adzanamiza mafumu a ku Israele.
15
Inunso anthu a ku Maresa, ndidzakutumirani adani kuti akugonjetseni. Akuluakulu a ku Israele adzabisala m'thanthwe la Adulamu.
16
Inu a ku Yuda, metani mpala, kuwonetsa kuti mukulira ana anu amene munkaŵakonda. Mukhale ndi dazi la dembo poti anawo adakusiyani, adatengedwa ku ukapolo.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7