bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Micah 5
Micah 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 6 →
1
Tsopano konzekani m'magulu ankhondo, inu a ku Yerusalemu. Atizinga ndi zithando zankhondo, akuthira nkhondo likulu la Israele.
2
Chauta akuti, “Koma iwe Betelehemu wa ku Efurata, inde ndiwe wamng'ono pakati pa mafuko a Yuda, komabe mwa iwe ndidzatulutsa munthu amene adzakhala wolamulira Israele. Iyeyo chiyambi chake nchakalekale, cha masiku amakedzana.”
3
Nchifukwa chake Mulungu adzasiya Israele mpaka pa nthaŵi yoti achire mkazi amene adzabale mwana. Pamenepo, otsala a mtundu wake adzabwereranso kwa Aisraele anzao.
4
Iye adzalimbikira, ndipo adzaŵeta nkhosa zake mwa mphamvu za Chauta ndi ulemerero wa dzina la Chauta, Mulungu wake. Ndipo iwo adzakhala mu mtendere, poti ukulu wake udzakhazikika pa dziko lonse lapansi.
5
Ndiye amene adzakhazikitse mtendere. Aasiriya akadzaloŵa m'dziko mwathu ndi kuyamba kutithira nkhondo, tidzaŵatumira atsogoleri ankhondo asanu ndi aŵiri kapena akalonga asanu ndi atatu.
6
Iwowo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga, dziko la Nimirodi adzalilamulira mwankhondo. Adzatipulumutsa kwa Aasiriya, iwowo akadzakaloŵa m'dziko mwathu, kudzatithira nkhondo.
7
Onse otsalira a Yakobe adzakhala dalitso pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochoka kwa Chauta. Adzakhala ngati mvula yowaza pa udzu, imene sichita kulamulidwa ndi anthu, siidikira lamulo la munthu.
8
Onse otsalira a Yakobe adzakhala temberero pakati pa mitundu ya anthu, ngati mkango pakati pa nyama zam'nkhalango. Adzakhala ngati mwana wa mkango, pakati pa gulu la nkhosa, amene amati akadzaziloŵerera, amazimbwandira ndi kuzikadzula. Ndipo sipakhala wozipulumutsa.
9
Inu Aisraele, mudzapambana adani anu, ndipo adani anu onsewo adzaonongeka.
10
Komabe Chauta akuuza Aisraele kuti, “Pa tsiku limenelo ndidzaononga akavalo anu onse, ndipo ndidzaphwasula magaleta anu.
11
Ndidzaononga mizinda ya m'dziko mwanu ndi kugwetseratu malinga anu.
12
Ndidzasakaza masenga anu onse, ndipo pakati panu sipadzakhalanso oombeza.
13
Ndidzaononga mafano anu onse pamodzi ndi miyala yoimika yopembedzerapo m'dziko mwanu. Simudzazigwadiranso zinthuzo zimene mudapanga ndi manja anu.
14
Ndidzagwetsa mafano anu a Asera m'dziko mwanu, ndipo ndidzaononga mizinda yake.
15
Mwaukali ndi mokwiya ndidzalanga mitundu yonse ya anthu imene sidandimvere.”
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
Recommended Reading
Commentary
Micah Commentaries
→
Devotional
Micah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→