bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Micah 2
Micah 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 3 →
1
Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo.
2
Akasirira minda, amailanda. Akakhumbira nyumba, amazilanda. Amavutitsa munthu ndi banja lake, naŵatengera zonse zimene ali nazo.
3
Nchifukwa chake zimene akunena Chauta ndi izi: “Imvani, ndidzakufitsirani tsoka chifukwa cha zoipa zonsezi. Ndidzakuvekani goli m'khosi mwanu, limene simungathe kulivula. Apo simudzayendanso monyada, chifukwa nthaŵi imeneyo idzakhala yoipa.
4
Tsiku limenelo anthu adzakupekerani nthano yokunyodolani, adzakuimbani nyimbo yamaliro, adzati, ‘Taonongeka kotheratu. Dziko limene Chauta adatigaŵira, bwanji afuna kutilanda! Minda yathu aigaŵira amene atigwira ukapolo.’ ”
5
Tsono pa nthaŵi imene Chauta adzabwezeranso dziko kwa anthu ake, inuyo simudzalandirako gawo lililonse.
6
Anthu amandiwuza kuti, “Musatilalikire, munthu asalalike zimenezi. Manyazi sadzatigwera ai.
7
Monga zoterezi nzoyenera kuzinena, inu a banja la Yakobe? Kodi kuleza mtima kwa Chauta kwatheratu? Kodi zimenezi nzimene adachita? Kodi mau ake sadzetsa zabwino kwa munthu woyenda molungama?”
8
Chauta akuti, “Koma inu mumaukira anthu anga ngati mdani. Mumaŵavula mkanjo anthu amtendere, amene amangoyenda ndi mtima wokhazikika, osaganizako za nkhondo.
9
Akazi a anthu anga mumaŵatulutsa m'nyumba zao zokoma. Ndipo ana ao mumaŵalanda madalitso anga kosalekeza.
10
Nyamukani, chokani, ano simalo opumulirapo. Zonyansa zanu zaŵaipitsa, zadzetsapo chiwonongeko choopsa.
11
Munthu wina atamapita uku ndi uku akulalika zabodza kuti, ‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’ mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde.
12
“Koma inu banja lonse la Yakobe, ndidzakusonkhanitsani. Onse otsala a ku Israele ndidzaŵasonkhanitsa pamodzi ngati nkhosa m'khola, ngati gulu la zoŵeta pa busa lake. Malowo adzakhala thithithi ndi chinamtindi cha anthu.”
13
Woŵapulumutsa adzaŵatsogolera, ndipo onse adzathyola pa chipata nathaŵa. Idzayambira ndi mfumu yao kudutsa, Chauta adzakhala patsogolo pao.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7