bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Micah 4
Micah 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 5 →
1
Pa masiku akudzaŵa, phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo.
2
Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe, ndipo adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tiziyenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.
3
Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko amphamvu, ngakhale akutali omwe. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.
4
Koma munthu aliyense azidzangodzikhalira mwamtendere patsinde pa mtengo wake wamphesa, ndi patsinde pa mkuyu wake. Palibe amene adzaŵachititsa mantha, pakuti mwiniwake, Chauta Wamphamvuzonse, wanena zimenezi.
5
Mitundu yonse ya anthu imayenda, uliwonse m'njira ya mulungu wake; koma ife tidzayenda m'njira ya Chauta, Mulungu wathu, mpaka muyaya.
6
Chauta akunena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzasonkhanitsa opuwala, ndidzakusa amene adachotsedwa kwao, ndiponso amene ndidaŵalanga.
7
Opundukawo ndidzaŵasandutsa anthu anga otsala, amene adachotsedwa kwao ndidzaŵasandutsa mtundu wamphamvu. Ine Chauta ndidzakhala mfumu yao pa phiri la Ziyoni, kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya.
8
“Tsono iwe Ziyoni, nsanja yotetezera nkhosa zanga, phiri la anthu anga, zimene ndidaakulonjeza zidzachitikadi. Ufumu wako wakale uja udzakubwereranso, Anthu a ku Yerusalemu ufumu wao uja udzafikanso.”
9
Kodi ukuliriranji mokuŵa chonchi mzinda iwe? Ukusaukiranji ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira? Kodi ndiye kuti ulibe mfumu, kapena phungu wokulangiza?
10
Muphiriphithe ndi kubuula, inu anthu a ku Ziyoni, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira. Pakuti tsopano mudzachoka mumzindamo, mukakhala mumidzi. Mudzachotsedwa kupita ku Babiloni. Komabe kumeneko mudzapulumutsidwa, kumeneko Chauta adzakuwombolani kwa adani anu.
11
Tsopano mitundu yambiri yasonkhana kuti imenyane ndi iwe Ziyoni. Ikunena kuti, “Tiyeni timuipitse, tiwone kutha kwake kwa mzinda wa Ziyoniwu.”
12
Koma anthuwo maganizo a Chauta saŵadziŵa, zimene Iye akukonzekera, iwo sazimvetsa. Sadziŵa kuti Iye waŵaunjika ngati mitolo ya tirigu pa malo opunthira.
13
Yamba kupuntha iwe Ziyoni, ndidzakusandutsa wamphamvu ngati nkhunzi ya nyanga zachitsulo, ngati nkhunzi ya ziboda zamkuŵa. Udzatswanya mitundu yambiri ya anthu, zimene adapindula udzazipereka kwa Chauta, chuma chao udzachipereka kwa Ambuye a dziko lonse lapansi.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
Recommended Reading
Commentary
Micah Commentaries
→
Devotional
Micah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→