bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Micah 7
Micah 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
1
Kalanga ine! Ndasanduka ngati wokunkha wosapeza zotsalira. Sipadatsalenso mphesa zoti nkudya. Sipadatsaleko nkhuyu zimene ndimazikonda.
2
Anthu abwino atha pa dziko lapansi, palibe ndi mmodzi yemwe wolungama. Onse akubisalirana mwachiwembu. Aliyense akusakira mbale wake mu ukonde.
3
Ndi akatswiri pochita zoipa. Akalonga ndi aweruzi amafuna ziphuphu, ndipo mtsogoleri amaŵauza zoipa zimene afuna kuti iwo achite. Motero amalakwira pamodzi.
4
Munthu wabwino koposa ali ngati lunguzi, wolungama koposa ndi wolasa ngati tchinga laminga. Lafika tsiku la chilango, limene alonda ao, aneneri, adanena. Lafika tsiku la chisokonezo chao.
5
Wina asakhulupirire mnansi, asadalire bwenzi lake lapamtima. Aliyense achenjere ndi pakamwa pake, ngakhale polankhula ndi mkazi wake yemwe.
6
Makono ana aamuna akunyoza atate ao, ana aakazi akuukira amai ao. Mtengwa akulongolozana ndi mpongozi wake, nkhondo ndi anansi.
7
Koma ine ndidzadalira Chauta. Ndidzaika mtima pa Mulungu Mpulumutsi wanga. Mulungu wanga adzandimva.
8
Inu adani athu musatiseke. Tidagwa inde, koma tidzadzukanso. Ngakhale tikhale mu mdima, Chauta ndiye nyale yathu.
9
Tachimwira Chauta, nchifukwa chake tiyenera kupirira mkwiyo wake, mpaka atazenga mlandu wathu ndi kuugamula. Koma pambuyo pake adzatiloŵetsa m'kuŵala, ndipo tidzaona chipulumutso chake.
10
Tsono adani athu adzaona zimenezi, ndipo manyazi adzaŵagwira anthu amene ankatifunsa kuti, “Ali kuti Chauta, Mulungu wanu?” Tidzaona kugonjetsedwa kwao, adzaponderezedwa ngati matope m'miseu.
11
Inu anthu a ku Yerusalemu, idzafikatu nthaŵi yomanganso malinga anu. Nthaŵi imeneyo malire anu adzafutuzidwa.
12
Nthaŵi imeneyo anthu anu adzabwerera kwa inu kuchokera ku Asiriya mpaka ku Ejipito, kuchokera ku Ejipito mpaka ku Mtsinje wa Yufurate, ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso, kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.
13
Koma dziko lapansi lidzasanduka chipululu chifukwa cha zoipa za anthu ake. Amenewo ndiwo malipiro a ntchito zao.
14
Inu Chauta muŵatsogolere anthu anu ndi ndodo yanu yoŵatetezera, muŵete nkhosa zanu zimene mudazisankha. Tsopano zikukhala zokha m'nkhalango pakati pa dziko la chonde. Koma muzilole kuti zikadye ku busa labwino, ku Basani ndi Giliyadi, monga masiku akale.
15
Chauta akuti, “Ndidzaŵaonetsa zodabwitsa, monga masiku amene ankatuluka ku Ejipito.”
16
Anthu a mitundu yambiri akadzaona zimenezo adzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzangogwira pakamwa, ndi kutseka makutu motaya mtima.
17
Adzavimvinizika pa dothi ngati njoka, ngati zolengedwa zina zokwaŵa. Adzabwera ali njenjenje kuchokera ku malinga ao. Moopa adzatembenukira kwa Inu Chauta, Mulungu wathu, ndipo adzachita nanu mantha.
18
Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika.
19
Mudzatichitiranso chifundo. Mudzapondereza pansi zolakwa zathu, mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja.
20
Mudzaonetsa kukhulupirika kwanu kwa Yakobe, ndi chikondi chanu chosasinthika kwa Abrahamu, monga mudalonjezera molumbira kwa makolo athu kuyambira pa masiku amakedzana.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
Recommended Reading
Commentary
Micah Commentaries
→
Devotional
Micah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→