bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Micah 6
Micah 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 7 →
1
Imvani tsopano zimene Chauta anene. Dzukani Ambuye, mufotokoze pamaso pa mapiri mlandu wanu. Magomo amve mau anu.
2
Imvani mlandu wa Chauta, inu mapiri, ndi inunso maziko amuyaya a dziko lapansi. Chautatu akuimba mlandu anthu ake, akutsutsana ndi Aisraele.
3
Chauta akuti, “Inu anthu anga, kodi ndakuchitani chiyani? Kodi ndakutopetsani nchiyani? Tandiyankhani!
4
Paja Ine ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito. Ndidakuwombolani ku dziko laukapololo. Ndipo ndidaachita kutuma Mose, Aroni ndi Miriyamu kuti akutsogolereni.
5
Inu anthu anga, kumbukirani zimene Balaki, mfumu ya ku Mowabu, adaafuna kukuchitani, ndiponso m'mene Balamu mwana wa Beori adamuyankhira. Kumbukirani zimene zidachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala. Kumbukirani zonsezi kuti muzindikire zimene Ine Chauta ndidachita pofuna kukupulumutsani.”
6
Kodi nditenge chiyani kuti ndifike pamaso pa Chauta, kuti ndikapembedze Mulungu Wakumwamba? Kodi nditenge anaang'ombe a chaka chimodzi kuti ndipereke nsembe zopsereza?
7
Kodi Chauta adzakondwera ndi nkhosa zamphongo zikwi zingapo kapena mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndidzapereke mwana wanga wachisamba chifukwa cha zolakwa zanga? Kodi mwana wanga adzakhale nsembe yolipira tchimo langa?
8
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
9
Ndi nzeru kuwopa dzina la Chauta. Akuuza mzinda wa Yerusalemu kuti, “Imvani, inu anthu onse okhala mumzinda muno.
10
Kodi Ine ndingathe kuiŵala chuma chimene chili m'nyumba za anthu oipa, chimene adachipata monyenga, ndiponso muyeso wopereŵera umene uli wotembereredwa?
11
Kodi ndingathe kulekerera munthu amene ali ndi sikelo zobera anzake ndiponso miyeso yonyenga?
12
Anthu olemera amachita zankhondo. Anthu onse ndi abodza, amangokhalira kunama.
13
Nchifukwa chake ndayambapo kukukanthani, kukuwonongani chifukwa cha machimo anu.
14
Mudzadya, koma simudzakhuta. Njala sidzakuchokani. Mudzakundika zinthu, koma sizidzasungika. Zimene mudzakundika zidzaonongedwa pa nkhondo.
15
Mudzabzala, koma simudzakolola, Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzaŵadzola. Mudzaponda mphesa, koma vinyo wake simudzamulaŵa.
16
Mwasunga machitidwe oipa a mfumu Omuri ndi ntchito zonse za banja la Ahabu. Mwatsata njira zao zonse. Motero ndidzakuwonongani kotheratu. Anthu a mitundu ina adzakunyodolani, kulikonse anthu adzakunyozani.”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7