bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Micah 3
Micah 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 4 →
1
Ine ndidati, “Imvani inu akuluakulu a Yakobe, olamulira a banja la Israele! Kodi oyenera kudziŵa chilungamo sindinu?
2
Mumadana ndi zabwino, mumakonda zoipa. Anthu anga mumaŵasenda amoyo, ndi kukangadzula mnofu wao.
3
Mumandidyera anthu anga, mumachita ngati kumaŵasenda, kuphwanya mafupa ao, ndi kumaŵachekera mumphika ngati nyama.
4
“Nthaŵi ikubwera pamene mudzalira kwa Chauta, koma sadzakuyankhani. Nthaŵi imeneyo adzakufulatirani chifukwa ntchito zanu nzoipa.”
5
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Pali aneneri amene amasokeza anthu anga: amamlosera za mtendere amene amaŵadyetsa, koma amamlosera nkhondo amene alibe choŵapatsa.”
6
Ndiye Chauta akuti, “Nchifukwa chake simudzaonanso zinthu m'masomphenya, simudzalosanso konse. Inu aneneri, kwakuderani, mdima wakugwerani.”
7
Alauli adzaŵanyazitsa, oombeza maula adzaŵachititsa manyazi. Onse adzangoti pakamwa gwirire, chifukwa Mulungu sakuŵayankha.
8
Koma ine Chauta wandidzaza ndi mphamvu, wandidzaza ndi mzimu wake. Wandidzaza ndi kulungama ndi kulimba mtima, kuti ndidzudzule a banja la Yakobe chifukwa cha zolakwa zao, kuti ndiwonetse Aisraele zoipa zao.
9
Imvani izi inu atsogoleri a banja la Yakobe, inu olamulira a banja la Israele. Inu mumadana ndi chilungamo, mumakhotetsa zinthu zokhoza.
10
Mumamanga Ziyoni ndi chuma chochipata pakupha anthu, Yerusalemu mumammanga ndi kuipa kwanu.
11
Atsogoleri ake saweruza popanda chiphuphu, ansembe ake saphunzitsa popanda malipiro, aneneri ake salosa popanda ndalama. Komabe amagonera pa Chauta ndi kunena kuti, “Kodi suja Chauta ali pakati pathu? Tsoka silingatigwere ai.”
12
Tsono chifukwa cha inu Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
Recommended Reading
Commentary
Micah Commentaries
→
Devotional
Micah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→