bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nehemiah 1
Nehemiah 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 2 →
1
Naŵa mau a Nehemiya, mwana wa Hakaliya: Pa mwezi wa Kisilevi, chaka cha 20 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, pamene ndinali mu mzinda wa Susa,
2
Hanani, mmodzi mwa abale anga, adabwera ndi anthu ena kuchokera ku Yuda. Ndipo ndidaŵafunsa za Yerusalemu ndiponso za Ayuda amene adaatsalirako osatengedwa ukapolo.
3
Adandiyankha kuti, “Anthu amene aja ali pa mavuto ndiponso ali ndi manyazi aakulu. Makoma a Yerusalemu ngogamukagamuka, ndipo zipata zake zidaonongeka ndi moto.”
4
Pamene ndidamva mau ameneŵa, ndidakhala pansi nkuyamba kulira, ndipo ndidalira masiku angapo. Ndinkasala chakudya, ndi kumapemphera kwa Mulungu wakumwamba.
5
Ndidati, “Inu Chauta, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, mumasunga chipangano. Mumaonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu amene amakukondani ndi kutsata malamulo anu.
6
Tsekulani maso ndipo tcherani khutu, kuti mumve pemphero la mtumiki wanune, limene ndikupereka tsopano kwa Inu usana ndi usiku, kupempherera Aisraele atumiki anu. Ndikuvomera machimo amene ife Aisraele tidakuchimwirani. Zoonadi, ine pamodzi ndi banja la makolo anga, tidakuchimwirani.
7
Tidakuchitirani zoipa zambiri, ndipo sitidamvere mau anu, malamulo anu ndiponso malangizo amene mudapatsa Mose mtumiki wanu.
8
Kumbukirani mau amene mudauza Mose mtumiki wanu akuti, ‘Ngati mukhala osakhulupirika, ndidzakumwazani pakati pa anthu a mitundu ina.
9
Koma mukabwerera kwa Ine, mukamvera malamulo anga ndi kuŵatsatadi, ndiye kuti ngakhale anthu anu omwazikawo akhale kutali chotani, ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse ndi kubwera nawo ku malo amene ndidasankha kuti azidzandipembedza kumeneko.’
10
Iwoŵa ndiwo atumiki anu ndi anthu anu amene mudaŵapulumutsa ndi mphamvu yanu yaikulu ndi dzanja lanu lolimba.
11
Inu Chauta, tcherani khutu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu ena amene amakonda kulemekeza dzina lanu. Lolani kuti ine mtumiki wanu zinthu zindiyendere bwino lero, ndipo kuti mfumu indichitire chifundo.” Pa nthaŵi imeneyo nkuti ine ndili woperekera zakumwa kwa mfumu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13