bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nehemiah 13
Nehemiah 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
1
Pa tsiku limenelo adaŵerenga buku la Mose, anthu onse alikumva. Ndipo adafika pa mau akuti, “Mwamoni kapena Mmowabu asaloŵe konse mu msonkhano wa Mulungu.
2
Paja ameneŵa sadapite kukakomana ndi ana a Aisraele, kuti akaŵapatse buledi ndi madzi. M'malo mwake adalemba Balamu kuti aŵatemberere. Komabe Mulungu wathu matembererowo adaŵasandutsa madalitso.”
3
Tsono pamene anthuwo adamva lamulolo, adachotsa anthu onse achilendo pakati pa gulu lao.
4
Koma zimenezi zisanachitike, wansembe Eliyasibu anali atasankhidwa kuti aziyang'anira zipinda zosungira katundu m'Nyumba ya Mulungu. Chifukwa chomvana ndi Tobiya, iyeyo
5
adakonzera Tobiyayo chipinda chachikulu m'mene kale ankasungiramo zopereka zaufa, lubani, ziŵiya, mphatso zoyenerera ansembe, ndiponso zopereka za chachikhumi cha chakudya, vinyo ndi mafuta, zimene adaalamula kuti azipatse Alevi, anthu oimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, potsata malamulo a Mose.
6
Pamene zimenezi zinkachitika ku Yerusalemu, nkuti ine palibe, popeza kuti pa chaka cha 32 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, mfumu ya ku Babiloni, ine ndidaapita kwa mfumuyo. Patapita nthaŵi ndithu, ndidapempha chilolezo kwa mfumu,
7
ndipo ndidabwereranso ku Yerusalemu. Tsono ndidapeza cholakwa chimene Eliyasibu adaachita pomkonzera Tobiya chipinda m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu.
8
Pamenepo ndidapsa mtima kwambiri, ndipo ndidamtaya kunja katundu yense wa Tobiya amene anali m'chipindamo.
9
Tsono ndidalamula kuti ayeretse zipindazo. Kenaka ndidabwezeranso ziŵiya za m'Nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi lubani.
10
Ndidapezanso kuti Alevi sankaŵapatsa magawo ao amene ankayenera kulandira. Choncho Aleviwo, pamodzi ndi anthu oimba nyimbo amene ankagwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, adathaŵa, aliyense kupita ku munda wake.
11
Choncho ndidaŵadzudzula akuluakulu aja kuti, “Kodi chifukwa chiyani Nyumba ya Mulungu yasiyidwa chonchi?” Ndipo ndidasonkhanitsa anthu aja ndi kuŵaikanso pa ntchito zimene ankazigwira
12
Nditachita zimenezi, Ayuda adayambanso kubwera ndi zopereka za chachikhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta, kuti azipereka ku nyumba zosungira chuma.
13
Ndipo ndidasankha aŵa kuti akhale asungachuma: wansembe Selemiya, mlembi Zadoki ndiponso Pedaya mmodzi mwa Alevi, kudzanso mthandizi wao Hanani, mwana wa Zakuri, mdzukulu wa Mataniya, popeza kuti ndidaadziŵa kuti anthuwo anali okhulupirika. Ntchito yao inali yogaŵira abale ao zinthu zofunika.
14
Inu Mulungu wanga, mundikumbukire ine pa zimenezi. Musaiŵale ntchito zanga zabwino zimene ndachitira Nyumba ya Mulungu wanga pofuna kumtumikira.
15
Nthaŵi imeneyo ndidaona anthu m'dziko la Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la sabata. Ena ankaunjika tirigu milumilu, nkumasenzetsa abulu. Enanso ankatenga vinyo, mphesa, nkhuyu, ndiponso katundu wa mtundu uliwonse, nkumabwera naye ku Yerusalemu, pa tsiku la sabata. Tsono ndidaŵachenjeza kuti asamagulitse chakudya pa tsiku la sabata.
16
Nawonso anthu ena a ku Tiro okhala mu Yerusalemu, ankabwera ndi nsomba ndi zamalonda za mtundu uliwonse, nkumazigulitsa pa tsiku la sabata kwa anthu a m'dziko la Yuda ndiponso kwa anthu okhala mu mzinda wa Yerusalemu.
17
Pomwepo ndidadzudzula atsogoleri a Ayuda, ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Monga simukuzindikira choipa chimene mukuchitachi pakuipitsa tsiku la sabata chonchi?
18
Makolo anu adachitanso motero momwemu, ndipo Mulungu wathu adadzetsa chiwonongeko pa ife ndi pa mzinda uno. Koma inu mukufuna kuutsanso mkwiyo wa Chauta pa Aisraele, pamene mukuipitsa tsiku la sabata motere.”
19
Nchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuziyamba kuda, tsiku la sabata lisanayambike, azitseka zipata zonse za Yerusalemu, ndipo asazitsekule mpaka tsiku la sabata litapita. Ndidaika antchito anga ena oyang'anira pa zipata, kuti katundu aliyense asaloŵe mumzindamo pa tsiku la sabata.
20
Motero anthu amalonda ogulitsa zinthu zamitundumitundu ankagona kunja kwa mzinda wa Yerusalemu kamodzi kapena kaŵiri konse.
21
Koma ndidaŵachenjeza ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Mukachitanso zimenezi ndidzakumangani.” Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka m'tsogolo mwake, anthuwo sadabwerenso pa tsiku la sabata.
22
Kenaka ndidaŵalamula Alevi kuti adziyeretse ndipo abwere kudzalonda pa zipata, kuti tsiku la sabata lisungike ngati lopatulika. Inu Mulungu wanga, mukumbukire zimenezinso pondikomera mtima, ndipo mundisunge potsata chikondi chanu chachikulu chosasinthika.
23
Nthaŵi imeneyo ndidaona Ayuda amene adaakwatira akazi a ku Asidodi, a ku Amoni ndiponso a ku Mowabu.
24
Mwakuti theka limodzi la ana ao ankalankhula chilankhulo cha ku Asidodi, sankathanso kulankhula Chiyuda, koma ankalankhula chilankhulo cha anthu a mitundu inayo.
25
Tsono ndidakangana nawo ndi kuŵatemberera. Ndidamenya ena mwa iwo ndi kuŵazula tsitsi. Ndipo ndidaŵalumbiritsa m'dzina la Mulungu kuti, “Musadzakwatitse ana anu aakazi kwa amuna achilendo, ndipo ana anu aamuna ndi inu nomwe musakwatire akazi achilendo.
26
Kodi Solomoni mfumu ya Aisraele suja adachimwa chifukwa cha akazi otereŵa? Pakati pa mitundu ya pansi pano panalibe mfumu yofanafana naye. Mulungu ankamkonda ndipo adamuika kuti akhale mfumu ya Aisraele onse. Komabe akazi achilendo adachimwitsa ngakhale iyeyo.
27
Monga tsopano tizimva kuti inunso mumachita choipa chachikulu chomwechi cha kuipira Mulungu pomakwatira akazi achilendo?”
28
Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe uja, anali atakwatira mwana wa Sanibalati wa ku Horoni. Nchifukwa chake ndidampirikitsa kuti achoke ku Yerusalemu.
29
Inu Mulungu wanga, mukumbukire m'mene anthuwo adaipitsira unsembe wao ndi m'mene adanyozera chipangano chimene mudachita ndi Alevi.
30
Umu ndimo m'mene ndidaŵayeretsera anthu poŵachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndidakhazikitsa ntchito za ansembe ndi za Alevi, kuti aliyense adziŵe bwino ntchito yake.
31
Chinanso, ndidalamula kuti nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha azipereke pa nthaŵi yoyenera. Inu Mulungu wanga, mukumbukire zonsezi ndipo mundikomere mtima.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13