bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nehemiah 5
Nehemiah 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 6 →
1
Tsono anthu ena pamodzi ndi akazi ao adayamba kudandaula kwambiri chifukwa cha Ayuda anzao.
2
Pakuti panali ena amene ankati, “Ife ndi ana athu tikuchuluka kwambiri, motero tikusoŵa tirigu wakudya, kuti tikhale ndi moyo.”
3
Panalinso ena amene ankati, “Ife tikuchita kupereka minda yathu, mitengo yathu yamphesa, pamodzi ndi nyumba zathu, ngati chikole, kuti tipeze tirigu, poti njala yatipha.”
4
Panali enanso amene ankati, “Ife tachita kukongola ndalama kuti tikhome msonkho wa minda yathu kwa mfumu, ndiponso kuti tikhomere mitengo yathu yamphesa.
5
Tsonotu ife ndi anzathu aja ndife amodzi, ndipo ana athu ngofanafana ndi ana ao. Komabe ifeyo tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo, mwakuti ana athu ena aakazi agwidwa kale. Ifeyo tilibe mphamvu zoti nkuchitapo kanthu, poti anthu aja atenga kale minda yathu ndi mitengo yathu yamphesa.”
6
Ine nditamva madandaulo amenewo, ndidapsa mtima kwambiri.
7
Ndidatsimikiza kuti ndichitepo kanthu, ndipo ndidaŵadzudzula atsogoleri ndi akulu olamula omwe. Ndidati, “Kodi nzokuwonerani kuti mukulipitsana chiwongoladzanja anthu apachibale nokhanokha!” Pamenepo ndidachititsa msonkhano waukulu kuti ndiŵazenge mlandu.
8
Tsiku limenelo ndidaŵauza kuti, “Monga m'mene kwathekera, tayesetsa kuwombola abale athu, Ayuda amene adaagulitsidwa ngati akapolo kwa anthu a mitundu ina. Koma tsopano inu mukugulitsa ngakhale abale anu omwe kwa anzao, kuti ife tiwumirizidwe kuŵaombola.” Anthuwo adangokhala chete osaona ponena.
9
Tsono ine ndidaonjeza kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwinotu ai. Muziwopa Mulungu ndi kumachita zolungama, kuti adani athu a mitundu inaŵa asapeze chifukwa chotinyozera.
10
Chinanso nchakuti ine, pamodzi ndi abale anga ndiponso antchito anga, tidaŵakongoza ndalama ndi tirigu. Tiyeni tisaŵaumirize kubwezera ngongolezo.
11
Muŵabwezere lero lomwe lino minda yao, mitengo yao yamphesa, mitengo yao ya olivi, ndi nyumba zao, ndipo muŵakhululukire ngongole za ndalama, za tirigu, za vinyo, ndi za mafuta, zimene mudaaŵakongoza.”
12
Ndiye iwowo adayankha kuti, “Tidzachitadi monga mukuneneramu. Tidzabwezera zimenezi osapemphapo kanthu.” Pamenepo ndidaitana ansembe, ndipo pamaso pao ndidaŵalumbiritsa akuluwo kuti adzachitedi monga momwe adalonjezera.
13
Tsono ndidakutumula chovala changa ndipo ndidanena kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu aliyense wosasunga malonjezo akeŵa. Amsandutse mmphaŵi pakumlanda nyumba yake, antchito ake ndi zonse zimene ali nazo.” Apo msonkhano wonse udavomereza ponena kuti, “Zikhale momwemo ndithu!” Ndipo onsewo adatamanda Chauta. Pambuyo pake akulu aja adachita monga m'mene adaalonjezera.
14
Kuyambiranso nthaŵi imene adandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa m'dziko la Yuda, kuchokera chaka cha 20 mpaka chaka cha 32 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, ndiye kuti zaka khumi ndi ziŵiri, ineyo ndi abale anga sitidalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa.
15
Abwanamkubwa amene analipo kale ankasautsa anthu pomaŵalanda chakudya ndi vinyo, ndi kuŵalipitsanso masekeli asiliva makumi anai. Ngakhale antchito ao nawonso ankathinitsa anthu. Koma ine sindidachite nawo zimenezo, popeza kuti ndinkaopa Mulungu.
16
Ndiponso ndinkakangamira pa ntchito yomanga makoma a mzinda, osafuna kupata minda. Antchito anga onsenso anali komweko, ndidaaŵalamula kuti adzipereke pa ntchito yokhayokhayo.
17
Komanso masiku onse ndinkadyetsa anthu 150, Ayuda ndi akulu olamula, kuphatikizapo anthu amene adaabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ina yotizungulira.
18
Tsono chakudya cha pa tsiku limodzi chinali ichi: ng'ombe imodzi, nkhosa zisanu ndi imodzi zonenepa, ndiponso nkhuku zochuluka. Pa masiku khumi aliwonse panalinso matumba achikopa ochuluka a vinyo. Komabe ngakhale choncho, ine sindidafune kulandira chakudya chimene abwanamkubwa ankalandira, chifukwa chakuti anthu anga anali othinidwa kwambiri.
19
Kuti tipeze bwino, kumbukirani, Inu Mulungu wanga, zonse zimene ndidaŵachitira anthuzi.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13