bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nehemiah 12
Nehemiah 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 13 →
1
Ansembe ndi Alevi, amene adabwerera pamodzi ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndiponso ndi Yesuwa, anali aŵa: Seraya, Yeremiya, Ezara,
2
Amariya, Maluki, Hatusi,
3
Sekaniya, Rehumu, Meremoti,
4
Ido, Ginetoyi, Abiya,
5
Miyamini, Maadiya, Biliga,
6
Semaya, Yoyaribu, Yedaya,
7
Salu, Amoki, Hilikiya, ndi Yedaya. Ameneŵa anali atsogoleri pakati pa ansembe ndi achibale ao pa nthaŵi ya Yesuwa.
8
Alevi anali aŵa: Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya ndi Yuda. Panalinso Mataniya, amene ankayang'anira za maimbidwe a nyimbo zachiyamiko, pamodzi ndi anzakewo.
9
Abale ao, Bakibukiya ndi Uni, ankaimba molandizana nawo pa nthaŵi ya chipembedzo.
10
Yesuwa adabereka Yoyakimu, Yoyakimu adabereka Eliyasibu, Eliyasibu adabereka Yoyada,
11
Yoyada adabereka Yonatani ndipo Yonatani adabereka Yaduwa.
12
Pa nthaŵi ya Yoyakimu, mkulu wa ansembe, atsogoleri a mabanja a ansembe anali aŵa: Mtsogoleri wa fuko la Seraya anali Meraya. Wa fuko la Yeremiya, anali Hananiya.
13
Wa fuko la Ezara anali Mesulamu, wa fuko la Amariya anali Yehohanani.
14
Wa fuko la Maluki anali Yonatani, wa fuko la Sebaniya anali Yosefe.
15
Wa fuko la Harimu anali Adina, wa fuko la Meraiyoti anali Helikai.
16
Wa fuko la Ido anali Zekariya, wa fuko la Ginetoni anali Mesulamu.
17
Wa fuko la Abiya anali Zikiri, wa fuko la Miniyamini, wa fuko la Mowadiya anali Pilitai.
18
Wa fuko la Biliga anali Samuwa, wa fuko la Semaya anali Yehonatani.
19
Wa fuko la Yoyaribu anali Matenai, wa fuko la Yedaya anali Uzi.
20
Wa fuko la Salai anali Kalai, wa fuko la Amoki anali Eberi.
21
Wa fuko la Hilikiya anali Hasabiya ndipo wa fuko la Yedaya anali Netanele.
22
Pa nthaŵi ya Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa, amene anali akulu a ansembe, padalembedwa maina a atsogoleri a mabanja a Alevi ndi a ansembe, mpaka pa nthaŵi imene mfumu Dariusi wa ku Persiya ankalamulira.
23
Adzukulu a Levi, makamaka atsogoleri a mabanja ao, adalembedwa m'buku la Mbiri, mpaka pa nthaŵi ya Yohanani mwana wa Eliyasibu.
24
Atsogoleri a Alevi, Hasabiya, Serebiya ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ankathandizana ndi abale ao poimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza, monga momwe Davide, munthu wa Mulungu, adaaŵalamulira kuti gulu liziimba molandizana ndi gulu linzake.
25
Mataniya, Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu, anali olonda nyumba zosungiramo chuma pa zipata za ku Nyumba ya Mulungu.
26
Ameneŵa ndiwo adaalipo pa nthaŵi ya Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndiponso pa nthaŵi ya bwanamkubwa Nehemiya ndi wansembe Ezara amene analinso katswiri wa malamulo.
27
Pamene anthu adati apereke kwa Mulungu khoma lozinga mzinda wa Yerusalemu, adaitana Alevi kuchokera konse kumene ankakhala, kuti abwere ku Yerusalemu kudzachita mwambo wopereka khomalo mokondwera, mothokoza ndiponso poimba pamodzi ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi mapangwe.
28
Tsono anthu a m'mabanja a Levi oimba nyimbo, adasonkhana pamodzi, kuchokera ku malo onse ozungulira Yerusalemu, ndiponso ku midzi ya Anetofati.
29
Kudabwera enanso ochokera ku Betegiligala, ku Geba, ndi ku Azimaveti, pakuti oimba nyimbo anali atamanga midzi yao pozungulira Yerusalemu.
30
Tsono ansembe ndi Alevi adachita mwambo wa kudziyeretsa. Mwambowu adachitiranso anthu, ndiponso zipata ndi khoma la mzinda.
31
Ineyo ndidadza nawo akuluakulu a ku dziko la Yuda ndipo ndidakwera nawo pa khoma. Ndidasankha magulu aŵiri mwa iwo, kuti aziyenda mu mdipiti ndi kumathokoza Mulungu. Mdipiti wina unkadzera cha ku dzanja lamanja pa khoma mpaka kukafika ku Chipata cha Kudzala.
32
Pambuyo pao pankadza Hosaya ndi theka la akuluakulu aja,
33
ndiponso Azariya, Ezara, Mesulamu,
34
Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya.
35
Ena mwa ana a ansembe amene ankaimba malipenga anali aŵa: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu.
36
Panali achibale ao aŵa: Semaya, Azarele, Milalai, Gilalai, Maai, Netanele, Yuda, ndi Hanani. Iwowo ankanyamula zoimbira zopangidwa ndi Davide, munthu wa Mulungu uja. Mlembi Ezara ndiye ankaŵatsogolera.
37
Kuchokera ku Chipata cha Kasupe, adakwera pa makwerero opita ku mzinda wa Davide, pa njira yotsatira khoma, chakumtunda kwa nyumba ya Davide, mpaka kukafika ku Chipata cha Madzi, kuvuma kwa mzinda wa Yerusalemu.
38
Mdipiti wina wa anthu othokoza Mulungu udadzera chakumanzere kwa khomalo, ndipo ine ndidautsata pambuyo, poyenda pa khoma pamodzi ndi theka lina la akuluakulu. Tidapitirira Nsanja ya Ng'anjo, kukafika ku Khoma Lotambasuka.
39
Tidadzeranso pa Chipata cha Efuremu, pa Chipata Chakale, pa Chipata cha Nsomba, pa Nsanja ya Hananele, pa Nsanja ya Zana, mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo potsiriza tidakaima ku Chipata cha Mlonda.
40
Choncho magulu othokoza aŵiri onsewo adakaimirira pafupi ndi Nyumba ya Mulungu. Pamodzi ndi ine ndi theka la akuluakulu aja,
41
panali ansembe aŵa akuimba malipenga: Eliyakimu, Maaseiya, Miniyamini, Mikaya, Eliyoenai, Zekariya ndi Hananiya.
42
Panalinso ansembe aŵa: Maaseiya, Semaya, Eleazara, Uzi, Yehohanani, Malikiya, Elamu ndi Ezero. Yezeraya ndiye ankatsogolera oimba nyimbo.
43
Pa tsiku limenelo anthu adapereka nsembe zochuluka, ndipo adakondwa kwakukulu, popeza kuti Mulungu ndiye adaŵakondwetsa. Akazi nawonso, pamodzi ndi ana, adakondwa, ndipo kukondwa kwa anthu a ku Yerusalemu kudamveka patali.
44
Tsiku limenelo padasankhidwa anthu oyang'anira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, ndi zopereka zachikhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka potsata Malamulo a Mose, kuti azipereka kwa ansembe ndi Alevi, kuchokera ku minda ya midzi yonse. Pakuti Ayuda ankakondwera nawo ansembe ndi Alevi otumikirawo,
45
chifukwa ankachita zimene Mulungu wao adaalamula, makamaka mwambo wopatulira zinthu. Oimba nyimbo ndiponso alonda a ku Nyumba ya Mulungu nawonso ankagwira ntchito zao potsata lamulo la Davide ndi Solomoni mwana wake.
46
Pa nthaŵi ya Davide ndi Asafu, panali mtsogoleri wa anthu oimba nyimbo, ndiponso panali nyimbo zotamanda ndi zothokoza Mulungu.
47
Pa nthaŵi ya Zerubabele ndi Nehemiya, anthu a m'dziko lonse la Israele ankapereka tsiku ndi tsiku mphatso zofunika kwa anthu oimba nyimbo ndiponso kwa alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankaikanso padera chigawo cha Alevi, ndipo Aleviwo nawonso ankaika padera chigawo cha ansembe, adzukulu a Aroni.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13