bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nehemiah 4
Nehemiah 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 5 →
1
Pamene Sanibalati adamva kuti tikumanga khoma, adapsa mtima nakalipa kwambiri, ndipo adayamba kuŵaseka Ayuda monyodola.
2
Adalankhula pamaso pa abale ake, ndi pamaso pa gulu lankhondo la ku Samariya, adati, “Kodi Ayuda achabechabeŵa akuchita chiyani? Monga amati nkumanganso mzindawu? Kodi nsembe ndiye adzapereka? Kodi adzaumaliza pa tsiku limodzi? Kodi adzachita kutolatolanso miyala yakale ija, ndi m'mene idapsera muja?”
3
Tobiya Mwamoni amene anali naye adati, “Inde, chimene akumangacho, ngati nkhandwe ikwerapo, idzagwetseratu khoma la miyala laolo.”
4
Pamenepo ndidayamba kupemphera, ndidati, “Inu Mulungu wathu, imvani m'mene akutinyozera. Mau ao otonza aŵabwerere, anthu ameneŵa alandidwe zao zonse, ndipo atengedwe ukapolo ku dziko lachilendo.
5
Musaŵakhululukire cholakwa chao, musafafanize tchimo lao, popeza kuti aputa ukali wanu pamaso pa amisiri omanga.”
6
Motero tidamangabe khoma, ndipo khoma lonse tidatha kulimanga mpaka theka la msinkhu wake, chifukwa chakuti anthu adaaikapo mtima pa ntchitoyo.
7
Koma pamene Sanibalati ndi Tobiya, ndiponso Arabu, Aamoni ndi Aasidodi adamva kuti ntchito yokonza makoma a Yerusalemu ikupita m'tsogolo, ndipo kuti malo ogamukagamuka aja akuŵakonzanso, adapsa mtima kwambiri.
8
Tsono adapangana za chiwembu choti akathire nkhondo Yerusalemu ndi kusokoneza anthu amumzindamo.
9
Apo ife tidapemphera kwa Mulungu wathu, ndipo tidaika alonda oti azititeteza kwa adani athuwo usana ndi usiku.
10
Tsono Ayuda ankati, “Mphamvu za onyamula zinyalala zilikutha, ndipo zinyalala zoyenera kutayidwazo nzambiri. Ndiyetu sitiitha ife ntchito yomanga khomayi.”
11
Adani athu ankanena zakuti ife Ayuda sitidzadziŵa kapena kuwona kanthu, mpaka iwo atafika pakati pathu, natipha ndi kuletsa ntchito yathuyi.
12
Tsono Ayuda okhala pafupi ndi adani athuwo ankabwera natichenjeza kakhumi konse kuti “Iwo aja adzafika kudzalimbana nanu kuchokera kulikonse kumene amakhala.”
13
Choncho paliponse pamene khomalo linali lisanathe, kumbuyo kwake, cha m'munsi mwake, m'malo okonza bwino, ndidaikamo anthu, m'mabanjam'mabanja, atatenga malupanga, mikondo ndi mauta.
14
Koma nditazindikira mantha ao, ndidachitapo kanthu. Mwakuti ndidauza atsogoleri ndi akulu olamula, ndiponso anthu ena onse kuti, “Musaŵaope ameneŵa. Kumbukirani kuti Chauta ndi wamkulu ndiponso ndi woopsa, tsono mumenyere nkhondo abale anu, ana anu, akazi anu, ndi nyumba zanu.”
15
Pamene adani athu adamva kuti ife tikudziŵa cholinga chao, adazindikira kuti Mulungu walepheretsa zimene iwowo adaapangana kuti atichite. Tsono tonse tidapitanso ku ntchito yomanga khoma, aliyense ku ntchito yake.
16
Kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake, theka lina la antchito anga linkagwira ntchitoyo, ndipo theka lina linkagwira mikondo, zishango, mauta ndiponso linkavala malaya achitsulo. Tsono akulu a Ayuda ankalimbitsa anthu ao amene ankamanga khoma.
17
Anthu onyamula zinyalala aja ankagwira ntchito ndi dzanja limodzi, kwinaku atagwira chida chankhondo.
18
Mmisiri aliyense anali atamangirira lupanga m'chiwuno mwake pamene ankamanga. Munthu woimba lipenga anali pambali panga nthaŵi zonse.
19
Ndidaŵauza atsogoleri ndi akuluakulu ndiponso anthu ena onse aja kuti, “Ntchitoyi njaikulu, ili pa dera lalikulu, ndipo ifeyo takhala motayanatayana kwambiri pa khoma.
20
Tsono kumene muliriko mukamva kulira kwa lipenga, mudzasonkhane msanga kumene tili ife kuno. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.”
21
Choncho enafe tinkagwira ntchito, ndipo theka lina la anthuwo linkagwira zida zankhondo, kuyambira m'matandakucha mpaka nyenyezi zitaoneka.
22
Pa nthaŵi imeneyi ndidaŵauzanso anthu kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone m'Yerusalemu, kuti tikhale ndi otitchinjiriza usiku, ndipo kuti masana tizigwira ntchito.”
23
Motero ine, anzanga, antchito anga, ndiponso anthu otitchinjiriza amene ankanditsata, panalibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene ankavula zovala zake usiku pogona. Aliyense ankasunga chida chankhondo pambalipa.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13