bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nehemiah 7
Nehemiah 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 8 →
1
Khoma la mzinda lija litamangidwa, ndidaikira zitseko, ndipo alonda a ku Nyumba ya Mulungu, anthu oimba nyimbo ndiponso Alevi adasankhidwa.
2
Pamenepo ndidasankha mbale wanga Hanani ndi Hananiya, mkulu woyang'anira linga lankhondo, kuti aŵiriwo azilamulira Yerusalemu. Hananiyayo anali munthu wokhulupirika ndi womvera Mulungu kupambana anthu ambiri.
3
Tsono ndidaŵauza kuti, “Musalole kuti atsekule zipata za Yerusalemu mpaka dzuŵa litatentha. Ndipo atseke zitseko ndi kuzipiringidza, alonda asanaŵeruke. Musankhe olonda pakati pa anthu okhala m'Yerusalemu, aliyense akhale pamalo pake, ndiponso akhale poyang'anana ndi nyumba yake.”
4
Mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu, koma anthu okhala mumzindamo anali oŵerengeka, ndipo munalibe nyumba zambiri.
5
Tsono Mulungu adaika mumtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse atsogoleri, akuluakulu ndiponso anthu onse, kuti alembedwe potsata mibadwo ya mabanja ao. Ndidapeza buku m'mene mudalembedwa maina a mabanja a anthu amene anali oyamba kubwerako ku ukapolo. Zolembedwa m'menemo zinali izi:
6
Naŵa anthu a m'chigawo cha Yuda amene adabwerako ku ukapolo, omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaaŵagwira kupita nawo ku Babiloni. Anthuwo adabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
7
Adabwera pamodzi ndi atsogoleri aŵa: Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana. Nachi chiŵerengero cha anthu aamuna a Aisraele.
8
A banja la Parosi 2,172.
9
A banja la Sefatiya 372.
10
A banja la Ara 652.
11
A banja la Pahatimowabu, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa ndi Yowabu 2,818.
12
A banja la Elamu 1,254.
13
A banja la Zatu 845.
14
A banja la Zakai 760.
15
A banja la Binuyi 648.
16
A banja la Bebai 628.
17
A banja la Azigadi 2,322.
18
A banja la Adonikamu 667.
19
A banja la Bigivai 2,067.
20
A banja la Adini 655.
21
A banja la Atere, ndiye kuti la Hezekiya, 98.
22
A banja la Hasumu 328.
23
A banja la Bezai 324.
24
A banja la Harifi 112.
25
A banja la Gibiyoni 95.
26
Amuna a ku Betelehemu ndi a ku Netofa 188.
27
Amuna a ku Anatoti 128.
28
Amuna a ku Betazimaveti 42.
29
Amuna a ku Kiriyati-Yearimu, Kefira, ndi Beeroti 743.
30
Amuna a ku Rama ndi Geba, 621.
31
Amuna a ku Mikimasi 122.
32
Amuna a ku Betele ndi Ai 123.
33
Amuna a ku Nebo wina 52.
34
A banja la Elamu wina 1,254.
35
A banja la Harimu 320.
36
A ku Yeriko 345.
37
A ku Lodi, Hadidi ndi Ono 721.
38
A ku Senaya 3,930.
39
Ansembe anali aŵa: a banja la Yedaya, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa, 973.
40
A banja la Imara 1,052.
41
A banja la Pasuri 1,247.
42
A banja la Harimu 1,017.
43
Alevi anali aŵa: a banja la Yesuwa ndi la Kadimiyele, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya, 74.
44
Oimba nyimbo anali aŵa: a banja la Asafu 148.
45
Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Salumu, a banja la Atere, a banja la Talimoni, a banja la Akubu, a banja la Hatita, a banja la Sobai, onse pamodzi 138.
46
Antchito a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Ziha, a banja la Hasufa, a banja la Tabaoti,
47
a banja la Kerosi, a banja la Siya, a banja la Padoni,
48
a banja la Lebana, a banja la Hagaba, a banja la Salimai,
49
a banja la Hanani, a banja la Gidele, a banja la Gahara,
50
a banja la Reaya, a banja la Rezini, a banja la Nekoda,
51
a banja la Gazamu, a banja la Uza, a banja la Paseya,
52
a banja la Besai, a banja la Meunimu, a banja la Nefusesimu,
53
a banja la Bakibuki, a banja la Hakufa, a banja la Harihuri,
54
a banja la Baziliti, a banja la Mehida, a banja la Harisa,
55
a banja la Barikosi, a banja la Sisera, a banja la Tema,
56
a banja la Neziya, a banja la Hatifa.
57
Mabanja a antchito ake a Solomoni anali aŵa: a banja la Sotai, a banja la Sofereti, a banja la Perida,
58
a banja la Yaala, a banja la Darikoni, a banja la Gidele,
59
a banja la Sefatiya, a banja la Hatili, a banja la Pokereti-Hazebaimu ndi a banja la Amoni.
60
Antchito onse a ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo zidzukulu za antchito a Solomoni, onse pamodzi analipo 392.
61
Anthu ali m'munsiŵa ndiwo amene adabwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni ndi ku Imeri, ngakhale sankatha kutsimikiza kuti makolo ao kapena mafuko ao analidi Aisraele enieni kapena ai.
62
A banja la Delaya, a banja la Tobiya, a banja la Nekoda 642.
63
Ndiponso ena mwa ansembe anali aŵa: a banja la Hobaya, a banja la Hakozi, a banja la Barizilai (kunena amene adaakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai wa ku Giliyadi, nkutenga dzina la bambo waoyo).
64
Iwoŵa adaafunafuna maina ao m'buku lolongosola kaundula wa mafuko ao, koma maina ao sadapezekemo. Choncho adaŵachotsa pa unsembe naŵaŵerenga kuti ngodetsedwa pa chipembedzo.
65
Bwanamkubwa adaŵauza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya choperekedwa kwa Mulungu, mpaka wansembe wodziŵa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu atapezeka.
66
Chiŵerengero cha anthu onse obwerako ku ukapolo aja chinali 42,360.
67
Kuwonjezera pamenepa, panalinso antchito ao aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Anali nawonso anthu oimba nyimbo, amuna ndi akazi omwe, okwanira 245.
68
Akavalo ao analipo 736, nyulu zao zinalipo 245,
69
ngamira zao zinalipo 435, ndipo abulu ao analipo 6,720.
70
Atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa adapereka ku thumba la chuma ndalama zagolide za makilogaramu asanu ndi atatu, mbale makumi asanu, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 530.
71
Atsogoleri ena a mabanja adapereka mosungira chumamo ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndiponso ndalama zasiliva za makilogaramu 1,250.
72
Ndipo anthu onse otsala adapereka ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndalama zasiliva zamakilogaramu 140, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 67.
73
Motero ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, anthu oimba nyimbo, ambiri mwa anthu wamba, atumiki a m'Nyumba ya Mulungu ndi Aisraele ena onse, ankakhala m'mizinda mwao.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13