bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nehemiah 8
Nehemiah 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 9 →
1
Ndipo anthu onse adasonkhana pamodzi pa bwalo la patsogolo pa Chipata cha Madzi. Tsono anthuwo adamuuza Ezara, amene anali mlembi, wansembe ndi mphunzitsi wa malamulo, kuti abwere ndi buku la Malamulo a Mose limene Chauta adaapatsa Israele.
2
Pamenepo Ezarayo adabwera ndi buku la Malamulolo, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, ku msonkhano wa amuna ndi akazi ndi ana amene ankatha kumvetsa zinthu bwino.
3
Tsono Ezara adaŵerenga bukulo atayang'ana bwalo la Chipata cha Madzi, kuyambira m'mamaŵa mpaka pa masana, pamaso pa amuna ndi akazi omwe, ndiponso onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Ndipo anthu onsewo ankatchera makutu kuti amve zoŵerengazo.
4
Mlembi Ezara adaaimirira pa nsanja yamitengo, imene anthuwo adaamanga chifukwa cha msonkhanowo. Ku dzanja lake lamanja kudaaimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseiya. Ku dzanja lake lamanzere kudaaimirira Pedaya, Misaele, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndiponso Mesulamu.
5
Tsono ataimirira pansanjapo, Ezara adafutukula buku, anthu onse akupenya. Pomwepo anthu onse adaimirira.
6
Kenaka Ezara adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wamkulu!” Ndipo anthu onse adakweza manja nayankha kuti, “Inde momwemo, inde momwemo.” Pambuyo pake adaŵeramitsa mitu pansi ndipo adapembedza Chauta ali chizyolikire.
7
Anthu ataimiriranso, Alevi adaŵathandiza kuti amvetse malamulo. Aleviwo anali aŵa: Yesuwa, Bani, Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani ndiponso Pelaya.
8
Aleviwo adaŵerenga buku la Malamulo a Mulungu momveka bwino, ndipo adatanthauzira mauwo kuti anthu amvetse bwino.
9
Tsono bwanamkubwa Nehemiya, pamodzi ndi Ezara wansembe ndi mphunzitsi wa malamulo, kudzanso Alevi amene ankaphunzitsa anthu, adauza anthu onse aja kuti, “Lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Ndiye kuti anthu onse ankalira atamva mau a Malamulowo.
10
Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”
11
Choncho Alevi adacheteketsa anthu onse naŵauza kuti, “Musalirenso ai, pakuti lero ndi tsiku loyera, choncho musakhale ndi chisoni.”
12
Pamenepo anthu onse adapita kwao kukadya ndi kumwa ndipo zakudya zina adagaŵirako anzao, kuti pakhale chikondwerero chachikulu, chifukwa chakuti tsopano anali atamvetsa bwino mau a Malamulo amene adaaŵerengedwawo.
13
Atsogoleri a mabanja, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, onse adabwera m'maŵa mwake kwa Ezara, mphunzitsi wa malamulo, kuti aphunzire mau a Malamulowo.
14
Tsono adapeza kuti m'buku la Malamulo mudalembedwa kuti Chauta adalamula kudzera mwa Mose kuti Aisraele azikhala m'zithando nthaŵi yonse ya chikondwerero cha pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri.
15
Motero adafalitsa ndi kulengeza m'midzi yao yonse ndiponso m'Yerusalemu, kuti, “Pitani ku mapiri, mukatengeko nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wakuthengo, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa, ndiponso za mitengo ina ya masamba ambiri, kuti mumangire misasa monga momwe zidalembedwera.”
16
Choncho anthuwo adapita nakatenga zonsezo ndipo aliyense adadzimangira misasa padenga pa nyumba yake, ndiponso m'mabwalo ao, m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, m'bwalo la pa Chipata cha Madzi ndi m'bwalo la pa Chipata cha Efuremu.
17
Motero onse amene adaasonkhana, ndiye kuti amene adaabwerako ku ukapolo, adamanga misasa, ndipo adakhala m'menemo. Kuyambira nthaŵi ya Yoswa, mwana wa Nuni, mpaka tsiku limenelo, Aisraele anali asanachitepo zoterozo. Motero kunali chikondwerero chachikulu kwambiri.
18
Tsiku ndi tsiku kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lotsiriza, Ezara ankaŵerenga buku la Malamulo a Mulungu. Anthu adachita chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu padachitika mwambo wotseka msonkhano, potsata buku la Malamulo lija.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13