bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Song of Solomon 1
Song of Solomon 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 2 →
1
Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse. Mkazi
2
Undimpsompsone ndi milomo yako, chifukwa chikondi chako nchoposa vinyo kukoma kwake.
3
Mafuta ako odzola ngonunkhira bwino, dzina lako likundikumbutsa za mafuta otsanyukako. Nchifukwa chaketu, atsikana sangaleke kukukonda.
4
Tenge, ndizikutsata, tiye tifulumire. Iwe mfumu yanga, kandiloŵetse m'chipinda mwako. Tizisangalala kwambiri ndi kukondwa limodzi. Chikondi chako tichitamande kupambana vinyo. Akazi onse amakukondera kaone!
5
Inu akazi a ku Yerusalemu, ine ndine wakuda inde, komatu wokongola tsono. Ndine wakuda ngati mahema a ku Kedara, komabe wokongola ngati makatani a m'nyumba ya Solomoni.
6
Musandiyang'ane monyoza chifukwa cha kudaku, ndi dzuŵatu lidandidetsali. Alongo anga adandikwiyira, mpaka kukandigwiritsa ntchito m'minda yamphesa. Koma munda wangawanga, osatha kuusamala.
7
Tandiwuza, iwe wokondedwa wanga wapamtima, kumene umadyetsa ziŵeto zako, kumene umazigoneka masana. Nanga ndizingokhala ndili zunguliruzunguliru ku magulu a ziŵeto za abusa anzako! Mwamuna
8
Iwe wokongola koposa akazi onsewe, ngati sukukudziŵa, uzingotsata m'makwalala a msambi wa ziŵeto, uzidyetsa mbuzi zako pambali pa mahema a abusawo.
9
Iwe bwenzi langa, kukongola kwako, ngati akavalo a magaleta a Farao.
10
Masaya ako akukongola ndi ndolo zam'makutuzi. Khosi lakonso likukongola ndi mikanda ya miyala yamtengowapatali.
11
Tidzakupangira ukufu wagolide, wokhala ndi timakaka tasiliva. Mkazi
12
Pamene mfumu inali gone podyera pake, mafuta anga onunkhira adapereka kafungo kachikoka.
13
Wokondedwa wanga ndikumuwona ngati kathumba ka mure, kamene kamakhala pakati pa maŵere angaŵa.
14
Wokondedwa wanga ndikumuwona ngati chipukutu cha maluŵa ofiira a m'munda wamphesa wa ku Engedi. Mwamuna
15
Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongola, ndiwe chiphadzuŵa. Maso ako akunga ngati nkhunda. Mkazi
16
Wokondedwa wanga, nawenso ndiwe wokongola, wokongoladi zedi. Malo athu ogonapo ndi msipu wobiriŵira.
17
Mitanda ya nyumba yathu ndi yamkungudza, phaso lake ndi la mtengo wa paini.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8