bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Song of Solomon 3
Song of Solomon 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 4 →
1
Usiku uliwonse ndili gone pabedi panga ndinkangomufunafuna amene mtima wanga umamkonda. Ndidamufunafuna koma osampeza. Ndidamuitana, koma iye osandiyankha.
2
Ndiye ndidati, “Ai, tsopano ndidzuka ndi kuloŵa mu mzinda, m'miseu ndi m'mabwalo. Ndimufunafuna amene mtima wanga umamkonda.” Ndidamufunafunadi, koma osampeza.
3
Alonda adandipeza pamene ankayendera mzinda. Ndidaŵafunsa kuti, “Kodi mwandiwonerako amene mtima wanga umamkonda?”
4
Ndidangoti iwo aja ntaŵapitirira pang'ono, ndampeza amene mtima wanga umamkonda. Ndidamgwira, osamlola kuti achoke, mpaka nditamloŵetsa m'nyumba ya amai anga, m'chipinda cha amene adandibala.
5
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, pali mphoyo ndi nswala zakuthengo, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Mkazi
6
Kodi nchiyaninso icho chikutulukira ku chipululucho ngati utsi watolotolo, chonunkhira mure ndi lubani, chokhala ndi zonunkhira zonse zogulitsa anthu amalonda?
7
Amenewo ndi machira a Solomoni. Pali ankhondo makumi asanu ndi limodzi, amuna anyonga a ku Israele operekeza.
8
Onsewo agwira malupanga, ndipo ngodziŵa kumenya nkhondo, aliyense wavala lupanga pambali pake, kuti alimbane ndi aupandu usiku.
9
Mfumu Solomoni adadzipangira machira a matabwa a ku Lebanoni.
10
Milongoti yake adapanga yasiliva, kumbuyo kwake kunali kwagolide, pampando pake panali nsalu yofiirira.
11
Tulukani, inu akazi a ku Ziyoni, mudzaone Mfumu Solomoni, atavala chisoti chaufumu chimene mai wake adamuveka pa tsiku la ukwati wake, tsiku limene mtima wake unkasangalala.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8