bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Song of Solomon 5
Song of Solomon 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 6 →
1
Ndaloŵa m'munda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga. Ndikukolola mure wanga ndi zokometsera chakudya. Ndikudya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe. Ndikumwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Akazi Inu apaubwenzi, idyani ndi kumwa: Inu okondana, imwani kwambiri! Mkazi
2
Kugona ndinagona, koma mtima wanga unali maso. Tamverani! Wokondedwa wanga akugogoda. Mwamuna “Tanditsekulira iwe mlongo wanga, iwe wokondedwa wanga, iwe nkhunda yanga, iwe wangwiro wanga. Mutu wanga wanyowa ndi mame, tsitsi langa lachita madzi chifukwa cha nkhungu yausiku.” Mkazi
3
Zovala ndavula kale, ndingazivalenso bwanji? Ndasamba kale m'miyendo, nanga ndiidetsenso poyenda?
4
Pamene wokondedwa wanga adangoti pisu dzanja pa chiboo chapachitseko, mtima wanga udachita kuti phwii!
5
Ndidanyamuka kukamtsekulira wokondedwa wanga, manja anga ali noninoni ndi mure. Zalazi zili mure chuchuchu pa zogwirira za mpiringidzo.
6
Ndidamtsekulira wokondedwa wanga, koma nkuti iyeyo atachokapo, atapita. Pamene iye ankalankhula, mtima wanga udangoti fumu! Ndidamfunafuna koma osampeza. Ndidamuitana, koma iye osandiyankha.
7
Alonda adandipeza pamene ankayendera mzinda. Adandimenya mpaka kundipweteka. Alonda apamalingawo adandilanda mwinjiro wanga.
8
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, mukampeza wokondedwa wangayo mumuuze kuti ine ndikumva chikondi chodwala nacho. Akazi
9
Iwe wokongola koposa akazi onsewe, kodi wokondedwa wakoyo ngwopambana wina aliyense bwanji? Kodi wokondedwa wakoyo ngwopambana ena onse chotani kuti uzichita kupemba motere? Mkazi
10
Wokondedwa wangayo ngwokongola, ndiponso wathanzi, wodziŵika zedi pakati pa amuna zikwi khumi.
11
Mutu wake uli ngati golide wosalala kwambiri. Tsitsi lake nlopotana bwino, lakuda bwino ngati nthenga za khwangwala.
12
Maso ake amaoneka okongola ngati nkhunda zitakhala pa akasupe a madzi, ngati nkhunda zitasamba mu mkaka, zitangoima bwinobwino.
13
Masaya ake ali ngati timinda ta mbeu zokometsera chakudya, zopatsa fungo lokoma. Milomo yake ili ngati akakombo, ili noninoni ndi zodzoladzola za mure.
14
Mikono yake ili ngati nthambi zagolide za makaka a miyala yamtengowapatali. Thupi lake nlosalala ngati mnyanga wanjovu woti aikamo miyala ya safiro.
15
Miyendo yake ili ngati mizati yamwala yokhazikika pa maziko agolide. Ali ndi maonekedwe aulemerero ngati mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe aulemu ngati mitengo ya paini ya pamapiripo.
16
Milomo yake njosangalatsa kwambiri, munthuyo amanditenga mtima kwabasi. Ameneyutu ndiye wokondedwa wanga, ndiponso bwenzi langa, inu akazi a ku Yerusalemu.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8