bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Song of Solomon 8
Song of Solomon 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
1
Ha! Achikhala unali mlongo wanga, woyamwa bere limodzi ndi ine! Ndikadakumana nawe panjira, bwenzi ntakumpsompsona, ndipo wina aliyense sakadandinyoza.
2
Ndikadakutenga nkukuloŵetsa m'nyumba ya amai anga, m'chipinda cha amene adandibala. Ndikadakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe, ndi madzi a makangaza.
3
Ine ndikadatsamira dzanja lako lamanzere, iwe nkundikumbatira ndi dzanja lamanja.
4
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Akazi
5
Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo, atatsamira wokondedwa wake? Mkazi Ndidakudzutsa patsinde pa mtengo wa apulosi uja. Pamenepo mpamene amai ako adachirira pokubala iweyo.
6
Umatirire mtima wako kuti musaloŵe winanso koma ine ndekha, ndipo sudzakumbatira winanso koma ine ndekha. Paja chikondi nchamphamvu ngati imfa, nsanje njaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti laŵilaŵi ngati malaŵi a moto, ndipo nchotentha koopsa.
7
Ngakhale madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, ngakhale madzi a chigumula sangachikokolole. Ngakhale munthu atapereka chuma chonse cha m'nyumba chifukwa chofuna kugula chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu. Alongo a Mkazi
8
Tili naye ife mlongo wathu wamng'ono, alibe ndi maŵere omwe. Tidzamchitira chiyani mlongo wathu pa tsiku limene adzamfunsire mbeta?
9
Iye akakhala ngati khoma, tidzammangira nsanja yasiliva. Koma akakhala ngati chitseko, tidzamchinga ndi matabwa amkungudza. Mkazi
10
Ine ndili ngati khoma, ndipo maŵere anga ali ngati nsanja zake. Tsono m'maso mwa wokondedwa wanga ndili ngati wodzetsa mtendere. Mwamuna
11
Solomoni anali ndi munda wamphesa ku Baala-Hamoni. Mundawo adaubwereka alimi. Aliyense mwa iwo ankayenera kupereka ndalama zasiliva chikwi chimodzi kuti azilimamo.
12
Koma munda wanga wamphesa ndi wangawanga, ndiponso wa ine ndekha. Iwe Solomoni, khala nazo ndalama chikwi chimodzi zija, khala nawonso alimi ako mazana aŵiri aja.
13
Iwe amene umakhala m'munda anzanga akumvetsera kuti amve liwu lako. Tandilola kuti ndilimve. Mkazi
14
Fulumiratu wokondedwa wanga, khala ngati mphoyo kapena ngati mwanawambaŵala wothamanga m'mapiri, m'mene mumamera mbeu zokometsera chakudya.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8