bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Song of Solomon 6
Song of Solomon 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 7 →
1
Iwe wokongola koposa akazi onsewe, kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti? Kodi wokondedwa wakoyo waloŵera potani, kuti tichite kukuthandiza kumfunafuna? Mkazi
2
Wokondedwa wanga watsikira kumunda kwakeku, ku timinda ta mbeu zokometsera chakudya. Akukadyetsa ziŵeto zake ku minda ndiponso akukathyola akakombo.
3
Wokondedwa wangayo ine ndine wake, ndipo iyeyo ndi wangawanga. Amadyetsa ziŵeto zake pakati pa akakombo. Mwamuna
4
Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongola ngati Tiriza, wa maonekedwe abwino ngati Yerusalemu, ndiwe wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili m'manja.
5
Usandipenyetsetse, pakuti maso ako amanditenga mtima. Tsitsi lako likuchita pekupeku ngati mbuzi, zoti zikutsetsereka pa mapiri a ku Giliyadi.
6
Mano ako ali mbee ngati nkhosa zometa, zoti angozisambitsa kumene. Mano onsewo ngoyang'anana bwino, palibe chigwelu nchimodzi chomwe.
7
Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo, masaya ako akuwoneka ngati mabandu a makangaza.
8
Mfumu ili ndi akazi enieni makumi asanu ndi limodzi, ili ndi akazi aang'ono makumi asanu ndi atatu, ilinso ndi anamwali tayetaye!
9
Koma ine nkhunda yanga, wangwiro wanga, ndi mmodzi yekha basi, mwana mmodzi yekha wa amai ake, mwana wapamtima wa amai ake. Anamwali atamuwona, adamutcha wodala. Akazi enieni a mfumu ndi akazi onse aang'ono adamtamanda.
10
Ndani uyu wooneka ngati mbandakuchayu, wokongola ngati mwezi, woŵala ngati dzuŵa, wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili m'manja?
11
Ndidatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi, kuti ndikayang'ane maluŵa akuchigwa, kuti ndikaone ngati mipesa idaphukira, ngati makangaza adachita maluŵa.
12
Ndisanazindikireko kanthu, ndidakhala ngati ndikulota kuti ndili m'galeta pambali pa mfumu yanga. Akazi
13
Bwerera, bwerera, iwe namwali wa ku Sulami, bwerera kuti tidzakupenyetsetse. Mkazi Chifukwa chiyani mukuti mudzandipenyetsetse ine Msulamine, pamene ndikuvina pakati pa magulu aŵiri?
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8