bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Song of Solomon 2
Song of Solomon 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 3 →
1
Ndili ngati duŵa la ku Saroni, ngati kakombo wam'zigwa. Mwamuna
2
Muja amakhalira kakombo pakati pa minga, ndi m'mene aliri wokondedwa wanga pakati pa atsikana. Mkazi
3
Muja umakhalira mtengo wa apulosi pakati pa mitengo yam'nkhalango, ndi m'mene aliri wokondedwa wanga pakati pa anyamata. Ndinkakondwa kwambiri ndikausa mumthunzi mwake, zipatso zake zinali tseketseketseke m'kamwamu.
4
Adanditenga kupita nane ku nyumba yaphwando, mbendera yake yozika pa ine inali chikondi.
5
Mundidyetse mphesa zouma, munditsitsimutse ndi maapulosi, pakuti ndikumva chikondi chodwala nacho.
6
Ha, ndidakakonda ineyo nditatsamira dzanja lake lamanzere, iyeyo nkundikumbatira ndi dzanja lamanja!
7
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, pali mphoyo ndi nswala zakuthengo, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Mkazi
8
Tamvani liwu la wokondedwa wanga! Taonani akubwera, akulumphalumpha pa mapiri, akujoŵajoŵa pa zitunda.
9
Wokondedwa wanga ali ngati mphoyo, kapena mwanawambaŵala. Si uyo waimirira apoyo, kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira m'mawindo, akuyang'anira pa made a mawindo.
10
Wokondedwa wanga akulankhula nkumandiwuza kuti: Mwamuna “Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, tiye tizipita.
11
Ona, nyengo yachisanu yatha, mvula yatha ndipo yapitiratu.
12
Maluŵa ayamba kuwoneka m'dziko, nthaŵi yoimba yafika, njiŵa zikumveka kulira m'dziko mwathu.
13
Mikuyu ikubereka zipatso, mipesa ikuyamba maluŵa. Mitengoyo ikutulutsa fungo lokoma. Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, tiye tizipita.
14
Iwe nkhunda yanga, yokhala m'ming'alu yam'matanthwe, yobisala m'phiri lotsetsereka, ntaonako nkhope yako, ntamvako liwu lako. Paja liwu lako nlomveka bwino, ndipo nkhope yako ndi yokongola.
15
Mutigwirire nkhandwe, nkhandwe zing'onozing'ono, zimene zimatiwonongera minda yamphesa, pakuti mipesa yathu idachita maluŵa.” Mkazi
16
Wokondedwa wangayo ndi wangadi, ndipo ine ndine wake. Amadyetsa gulu lake la ziŵeto pakati pa akakombo.
17
Kamphepo kamadzulo kakamayamba kuuzira, mithunzi ikamayamba kuthaŵa, unyamuke, iwe wokondedwa wanga, uthamange ngati mphoyo, kapena ngati mwanawambaŵala pakati pa mapiri azigwembezigwembe.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8