bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Song of Solomon 4
Song of Solomon 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 5 →
1
Ndiwe wokongola, iwe wokondedwa wanga! Ndithuditu, ndiwe wokongoladi! Kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo maso ako akuwoneka oŵala ngati nkhunda. Tsitsi lako likuchita pekupeku ngati mbuzi zoti zikutsetsereka pa mapiri a ku Giliyadi.
2
Mano ako ali mbee ngati nkhosa zometa zoti angozisambitsa kumene. Mano onsewo ngoyang'anana bwino, palibe chigwelu nchimodzi chomwe.
3
Milomo yako ili ngati mbota yofiira, ndipo pakamwa pako mpokongola zedi. Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo, masaya ako, akuwoneka ngati mabandu a makangaza.
4
Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndipo yosalala. Mkanda wako wam'khosi, ngati zishango 1,000 zokoloŵeka kuzungulira nsanjayo.
5
Maŵere ako ali ngati mbaŵala ziŵiri, ngati mphoyo zamapasa zimene zikudya pakati pa akakombo.
6
Pamene kamphepo kamadzulo kakuyamba kuuzira, ndipo mithunzi ikuthaŵa, ndidzapita mofulumira ku phiri la mure, ndi ku chitunda cha lubani.
7
Ndiwe wokongola kwabasi, iwe wokondedwa wanga. Ulibe nkachilema komwe.
8
Tiye tichokeko ku Lebanoni, iwe mkazi wanga. Tiye tichoke ku Lebanoni kuno, utsagane ndi ine. Utsikepo pa nsonga ya phiri la Amana, pa nsonga ya phiri la Seniri ndi la Heremoni. Uchokemo m'mapanga a mikango, uchokeko ku ngaka za akambuku.
9
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, wangoti mtima wangawu kwe! Wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi mphande imodzi ya mkanda wa m'khosi mwako.
10
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, chikondi chako nchosangalatsa. Chikondi chako nchosangalatsa kupambana vinyo, mafuta ako ndi onunkhira bwino kupambana zonunkhira zabwino zonse.
11
Iwe mkazi wanga, milomo yako ili uchi mvee! Kunsi kwa lilime lako kuli ngati uchi ndi mkaka. Fungo la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.
12
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, uli ngati munda wopiringidza, ngati munda wopiringidza, ngati kasupe wochingidwa.
13
Kumeneko mbeu zimakondwa bwino. Munda wake, ngati dimba la makangaza lokhalanso ndi zipatso zokoma zamitundumitundu, ndi maluŵa amitundumitundu.
14
Kuli mitengo ndi zitsamba zosiyanasiyana zopangira zonunkhira zabwino kwambiri.
15
Iwe uli ngati kasupe wothirira munda, ngati chitsime cha madzi abwino, ngati mitsinje yamadzi yochokera ku Lebanoni. Mkazi
16
Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, bwera kuno, iwe mphepo yakumwera. Uuzire pa munda wanga kuti fungo lake lokoma likwanire ponseponse. Wokondedwa wanga aloŵe m'munda mwake, adye zipatso zake zokoma.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8