bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jeremiah 10
Jeremiah 10
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 11 →
1
Tamvani mau amene Yehova anena kwa inu, nyumba ya Israyeli;
2
atero Yehova, a Musaphunzire njira ya amitundu, musaope zizindikiro za m'thambo; pakuti amitundu aziopa izo.
3
Pakuti miyambo ya anthu iri yacabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, nchito ya manja a mmisiri ndinkhwangwa.
4
Aukometsa ndi siliva ndi golidi; aucirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike.
5
Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kucita coipa, mulibenso mwa iwo kucita cabwino.
6
Cifukwa palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkuru, ndipo dzina lanu liri lalikuru ndi lamphamvu,
7
Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu.
8
Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo cilangizo, copanda pace.
9
Abwera ndi siliva wa ku Tarisi, wosulasula wopyapyala ndi golidi wa ku Ufazi, nchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zobvala zao ndi nsaru ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi nci ito za muomba.
10
Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wace dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wace.
11
Muzitero nao, milungu imene sinalenga miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha ku dziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo.
12
Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yace, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yace, nayala thambo ndi kuzindikira kwace;
13
polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, naturutsa mphepo m'zosungira zace.
14
Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lace losemasema; pakuti fanizo lace loyenga liri bodza, mulibe mpweya mwa iwo.
15
Ndiwo cabe, ndiwo ciphamaso; pa nthawi ya kulangidwa kwao adzatha.
16
Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti iye ndiye analenga zonse; Israyeli ndiye mtundu wa colowa cace; dzina lace ndi Yehova wa makamu.
17
Nyamula katundu wako, iwe wokhala m'linga.
18
Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire.
19
Tsoka ine, ndalaswa! bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu bvuto langa ndi ili, ndipirire nalo.
20
Hema wanga waonongeka, zingwe zanga zonse zaduka; ana anga aturuka mwa ine, palibe iwo; palibenso amene adzamanga hema wanga, kapena kucinga nsaru zanga,
21
Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; cifukwa cace sanapindula; zoweta zao zonse zabalalika.
22
Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikuru lituruka m'dziko la kumpoto, likacititse midzi ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe.
23
Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ace.
24
Yehova, mundilangize, koma ndi ciweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti.
25
Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwace.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52