bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jeremiah 46
Jeremiah 46
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 47 →
1
Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri akunena za amitundu.
2
Za Aigupto: kunena za nkhondo ya Farao-neko mfumu ya Aigupto, imene inali pa nyanja ya Firate m'Karikemisi, imene anaikantha Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda.
3
Konzani cikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo.
4
Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zacitsulo; tuulani nthungo zanu, bvalani malaya acitsulo.
5
Cifukwa canji ndaciona? aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osaceukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.
6
Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pa nyanja ya Firate wapunthwa nagwa.
7
Ndani uyu amene auka ngati Nile, madzi ace ogabvira monga nyanja?
8
Aigupto auka ngati Nile, madzi ace agabvira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ace.
9
Kwerani, inu akavalo; citani misala, inu magareta, aturuke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira cikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.
10
Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza cilango, kuti abwezere cilango adani ace; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa nyanja ya Firate.
11
Kwera ku Gileadi, tenga bvunguti, namwali iwe mwana wa Aigupto; wacurukitsa mankhwala cabe; palibe kucira kwako.
12
Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kupfuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.
13
Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo adzafika adzakantha dziko la Aigupto.
14
Nenani m'Aigupto, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.
15
Akulimba ako akokoledwa bwanji? sanaime, cifukwa Yehova anawathamangitsa,
16
Anapunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzace, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, ku dziko la kubadwa kwathu, kucokera ku lupanga lobvutitsa.
17
Ndipo anapfuula kumeneko, Farao mfumu ya Aigupto ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira,
18
Pali Ine, ati Mfumu, dzina lace ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimeli pambali pa nyanja, momwemo adzafika.
19
Mwana wamkazi iwe wokhala m'Aigupto, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsya, mulibenso wokhalamo.
20
Aigupto ndi ng'ombe ya msoti yosalala; cionongeko cituruka kumpoto cafika, cafika.
21
Ndiponso olipidwa ace ali pakati pace onga ngati ana a ng'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.
22
Mkokomo wace udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo.
23
Adzatema nkhalango yace, ati Yehova, pokhala yosapitika; pakuti acuruka koposa dzombe, ali osawerengeka.
24
Mwana wace wamkazi wa Aigupto adzacitidwa manyazi, adzaperekedwa m'manja a anthu a kumpoto.
25
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, ati: Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Aigupto, pamodzi ndi milungu yace, ndi mafumu ace; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;
26
ndipo ndidzawapereka m'manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndi m'manja a atumiki ace; pambuyo pace adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova.
27
Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usacite mantha, iwe Israyeli: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kucokera kutari, ndi mbeu yako ku dziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m'mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye,
28
Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndiri ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi ciweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 47 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52