bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jeremiah 39
Jeremiah 39
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 40 →
1
Caka cacisanu ndi cinai ca Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo ndi nkhondo yace yonse, ndi kuumangira misasa.
2
Caka cakhumi ndi cimodzi ca Zedekiya, mwezi wacinai, tsiku lacisanu ndi cinai, mudzi unabooledwa.
3
Ndipo akuru onse a mfumu ya ku Babulo analowa, nakhala m'cipata capakati, Nerigalisarezara, Samgari Nebo, Sarisekimu, mkuru wa adindo, Nerigalisarezara mkuru wa alauli ndi akuru ena onse a mfumu ya ku Babulo.
4
Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa naturuka m'mudzi usiku, panjira pa munda wa mfumu, pa cipata ca pakati pa makoma awiri; ndipo iye anaturukira pa njira ya kucidikha.
5
Koma nkhondo ya Akasidi inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo ku Ribila m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.
6
Pamenepo mfumu ya ku Babulo inapha ana a Zedekiya ku Ribila pamaso pace; mfumu ya ku Babulo niphanso aufulu onse a Yuda.
7
Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, nammanga m'zigologolo, kunka naye ku Babulo.
8
Ndipo Akasidi anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.
9
Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mudzi, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babulo.
10
Koma aumphawi a anthu, amene analibe kanthu, Nebuzaradani kapitao wa alonda anawasiya m'dziko la Yuda, nawapatsa mipesa ndi minda nthawi yomweyo.
11
Ndipo Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anamuuza Nebuzaradani kapitao wa alonda, za Yeremiya, kuti,
12
Umtenge, numyang'anire bwino, usamsautse, koma umcitire monga iye adzanena nawe.
13
Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkuru wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Nerigalisarezari mkuru wa alauli, ndi akuru onse a mfumu ya ku Babulo;
14
iwonso anatumiza, namcotsa Yeremiya m'bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu.
15
Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, potsekeredwa iye m'bwalo la kaidi, kuti,
16
Pita, ukanene kwa Ebedi-Meleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taona, ndidzafikitsira mudzi uwu mau anga kuusautsa, osaucitira zabwino; ndipo adzacitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.
17
Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa.
18
Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo sudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nao moyo wako ngati cofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine, ati Yehova.
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 40 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52