bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jeremiah 14
Jeremiah 14
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 15 →
1
Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya onena za cirala.
2
Yuda alira, ndipo zipata zace zilefuka, zikhala pansi zobvekedwa ndi zakuda; mpfuu wa Yerusalemu wakwera.
3
Akuru ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, apfunda mitu yao.
4
Cifukwa ca nthaka yocita ming'aru, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, apfunda mitu yao.
5
Inde, nswalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ace, cifukwa mulibe maudzu.
6
Mbidzi zinaima pamapiri oti se, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, cifukwa palibe maudzu.
7
Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, citani Inu cifukwa ca dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zacuruka; takucimwirani Inu.
8
Inu, ciyembekezo ca Israyeli, mpulumutsi wace nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?
9
Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, tichedwa ndi dzina lanu; musatisiye.
10
Atero Yehova kwa anthu awa, Comwecoakonda kusocerera; sanakaniza mapazi ao; cifukwa cace. Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira coipa cao, nadzalanga zocimwa zao.
11
Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino.
12
Pamene asala cakudya, sindidzamva kupfuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi cirala, ndi caola.
13
Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi cirala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.
14
Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi cinthu cacabe, ndi cinyengo ca mtima wao.
15
Cifukwa cace atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatuma, koma ati, Lupanga ndi cirala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi cirala aneneriwo adzathedwa.
16
Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu cifukwa ca cirala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna ndi akazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.
17
Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukuru, ndi bala lopweteka kwambiri.
18
Ndikaturukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! ndikalowa m'mudzi, taonani odwala ndi njala pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.
19
Kodi mwakanadi Yuda? kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? bwanji mwatipanda ife, ndipo tiribe kucira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakucira, ndipo taonani mantha!
20
Tibvomereza, Yehova, cisalungamo cathu, ndi coipa ca makolo athu; pakuti takucimwirani Inu.
21
Musatinyoze ife, cifukwa ca dzina lanu; musanyazitse mpando wacifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.
22
Mwa zacabe za mitundu ya anthu ziripo kodi, zimene zingathe kubvumbitsa mvula? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52