bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jeremiah 4
Jeremiah 4
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 5 →
1
Ngati udzabwera, Israyeli, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzacotsa zonyansa zako pamaso panga sudzacotsedwa.
2
Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'ciweruziro, ndi m'cilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.
3
Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.
4
Mudzidulire nokha kwa Yehova, cotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala m'Yerusalemu; ukali wanga ungaturuke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe anu.
5
Nenani m'Yuda, lalikirani m'Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; pfuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'midzi ya malinga.
6
Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi coipa cocokera kumpoto ndi kuononga kwakukuru.
7
Mkango wakwera kuturuka m'nkhalango mwace, ndipo woononga amitundu ali panjira, waturuka m'mbuto mwace kuti acititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo.
8
Pamenepo, bvalani ciguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wakuopsya wa Yehova sunabwerera pa ife.
9
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzatayika, ndi mitima ya akuru; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa.
10
Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mu'dzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.
11
Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yocokera ku mapiri oti se m'cipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosaungula, yosayeretsa;
12
mphepo yolimba yocokera kumeneko idzandifika ine; tsopanonso ndidzaweruza iwo maweruzo.
13
Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magareta ace ngati kabvumvulu; akavalo ace athamanga kopambana mphungu, Tsoka ife! pakuti tapasuka.
14
Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kucotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako acabe agona mwako masiku angati?
15
Pakuti mau anena m'Dani nalalikira nsautso m'phiri la Efraimu:
16
Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira ku dziko lakutari, nainenera midzi ya Yuda mau ao.
17
Monga adindo a m'munda amzinga iye; cifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.
18
Njira yako ndi nchito zako zinakucitira izi; ici ndico coipa cako ndithu; ciri cowawa ndithu, cifikira ku mtima wako.
19
Matumbo anga, matumbo anga! ndipoteka pamtima panga peni peni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.
20
Alalikira cipasuko cilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsaru zanga zocinga m'kamphindi.
21
Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga?
22
Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ocenjera kucita coipa koma kucita cabwino sakudziwa.
23
Ndinaona dziko lapansi, ndi rpo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika.
24
Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka.
25
Ndinaona, ndipo taona, panalibe munthu, ndi mbalame zonse zakumwamba zinathawa.
26
Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali cipululu, ndipo midzi yace yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wace woopsya.
27
Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.
28
Cifukwa cimeneco dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; cifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.
29
Mudzi wonse uthawa m'phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m'nkhalango, adzakwera pamiyala; midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m'menemo.
30
Nanga iwe, udzacita ciani pamene udzafunkhidwa? Ngakhale udzibveka ndi zofiira, ngakhale udzibveka ndi zokometsera zagolidi, ngakhale udzikuzira maso ako ndi kupaka, udzikometsera pacabe; mabwenzi adzakunyoza adzafuna moyo wako.
31
Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wace woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ace, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! pakuti moyo wanga walefuka cifukwa ca ambanda.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52