bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jeremiah 16
Jeremiah 16
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 17 →
1
Ndiponso mau a Mulungu anadza kwa ine, kuti,
2
Usatenge mkazi, usakhale ndi ana amuna ndi akazi m'malo muno.
3
Pakuti Yehova atero za ana amuna ndi za ana akazi akubadwa m'malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m'dziko muno:
4
Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala cakudya ca mbalame za kumlengalenga, ndi zirombo za dziko lapansi.
5
Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukacita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndacotsa mtendere wanga pa anthu awa, cifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.
6
Akuru ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzacita maliro ao, sadzadziceka, sadzadziyeseza adazi, cifukwa ca iwo;
7
anthu sadzawagawira mkate pamaliro, kuti atonthoze mitima yao cifukwa ca akufa, anthu sadzapatsa iwo cikho ca kutonthoza kuti acimwe cifukwa ca atate ao kapena mai wao.
8
Usalowe m'nyumba ya madyerero kukhala nao, ndi kudya ndi kumwa.
9
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi.
10
Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Cifukwa cace nciani kuti Yehova watinenera ife coipa cacikuru ici? mphulupulu yathu ndi yanji? cimo lathu lanji limene tacimwira Yehova Mulungu wathu?
11
Pamenepo uziti kwa iwo, Cifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu yina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga cilamulo canga;
12
ndipo mwacita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wace woipa, kuti musandimvere Ine;
13
cifukwa cace ndidzakuturutsani inu m'dziko muno munke ku dziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu yina usana ndi usiku, kumene sindidzacitira inu cifundo.
14
Cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova, kuti sadzanenanso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kuwaturutsa m'dziko la Aigupto.
15
Koma, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kucokera ku dziko la kumpoto, ndi ku maiko ena kumene anawapitikitsirako; ndipo ndidzawabwezanso ku dziko lao limene ndinapatsa makolo ao.
16
Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pace ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.
17
Pakuti maso anga ali pa njira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga,
18
Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi cimo lao cowirikiza; cifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza colowa canga ndi zonyansa zao.
19
Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kucokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira colowa ca bodza lokha, zopanda pace ndi zinthu zosapindula nazo.
20
Kodi munthu adzadzipangira yekha milungu, imene siiri milungu?
21
Cifukwa cace, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52