bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jeremiah 42
Jeremiah 42
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 43 →
1
Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi Jezaniya mwana wace wa Hosiya, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono, kufikira wamkuru, anayandikira,
2
nati kwa Yeremiya mneneri, Cipembedzero cathu cigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Ambuye Mulungu wanu, cifukwa ca otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;
3
kuti Yehova Mulungu wanu atisonyeze ife njira imene tiyendemo, ndi comwe ticite.
4
Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti ciri conse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.
5
Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati siticita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.
6
Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.
7
Ndipo panali atapita masiku khumi, mau a Yehova anadza kwa Yeremiya.
8
Ndipo anaitana Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru,
9
nati kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, kwa Iye amene munandituma ine ndigwetse pembedzero lanu pamaso pace,
10
Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa naco cisoni coipa cimene ndakucitirani inu.
11
Musaope mfumu ya ku Babulo, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndiri ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m'dzanja lace.
12
Ndipo ndidzakucitirani inu cifundo, li kuti iye akucitireni inu cifundo, nakubwezereni inu ku dziko lanu.
13
Koma mukati, Sitidzakhala m'dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu;
14
ndi kuti, Iai; tidzanka ku Aigupto, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;
15
cifukwa cace mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe m'Aigupto, kukakhala m'menemo;
16
pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Aigupto, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Aigupto; pamenepo mudzafa.
17
Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Aigupto kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku coipa cimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.
18
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Aigupto; ndipo mudzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo; ndipo simudzaonanso malo ano.
19
Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe m'Aigupto; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero.
20
Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzacita.
21
Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamva mau a Yehova Mulungu wanu m'cinthu ciri conse cimene Iye wanditumira ine naco kwa inu.
22
Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi caola, komwe mufuna kukakhalako.
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 43 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52