bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jeremiah 22
Jeremiah 22
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 23 →
1
Yehova atero: Tsikira ku nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi kunena komweko mau awa,
2
ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.
3
Yehova atero: Citani ciweruzo ndi cilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musacite coipa, musamcitire mlendo ciwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosacimwa pamalo pano.
4
Pakuti ngati mudzacitadi ici pamenepo, padzalowa pa zipata za nyumba iyi mafumu okhala pa mpando wacifumu wa Davide, okwera m'magareta ndi pa akavalo, iye, ndi atumiki ace, ndi anthu ace.
5
Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.
6
Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Gileadi, ndi mutu wa Lebano; koma ndidzakuyesa iwe cipululu, ndi midzi yosakhalamo anthu.
7
Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zace; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m'moto.
8
Ndipo amitundu ambiri adzapita pa mudzi uwu, nadzati yense kwa mnzace, Yehova anatero nao mudzi waukuru uwu cifukwa ninji?
9
Ndipo adza yankha, Cifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu yina, ndi kuitumikira.
10
Musamlirire wakufa, musacite maliro ace; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.
11
Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwace mwa Yosiya atate wace, amene anaturuka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iri yonse;
12
koma kumene anamtengera iye ndende, kumeneko adzafa, ndipo sadzaonanso dziko ili.
13
Tsoka iye amene amanga nyumba yace ndi cisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi cosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzace nchito osamlipira, osampatsa mphotho yace;
14
amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikuru, nadziboolera mazenera; nabvundima chindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.
15
Kodi udzakhala mfumu, cifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadya ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? kumeneko kunamkomera.
16
Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? ati Ambuye.
17
Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosacimwa, ndi kusautsa, ndi zaciwawa, kuti uzicite.
18
Cifukwa cace Yehova atero za Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! kapena, Kalanga ine ulemerero wace!
19
Adzamuika monga kuika buru, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata za Yerusalemu.
20
Kwera ku Lebano, nupfuule; kweza mau ako m'Basani; nupfuule m'Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha,
21
Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvera mau anga,
22
Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m'ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa cifukwa ca coipa cako conse.
23
Iwe wokhala m'Lebano, womanga cisa cako m'mikungudza, udzacitidwa cisoni cacikuru nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!
24
Pali ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wace wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya pa dzanja langa lamanja, ndikadacotsa iwe kumeneko;
25
ndipo ndidzakupereka iwe m'dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m'dzanja la iwo: amene uwaopa, m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, m'dzanja la Akasidi.
26
Ndipo ndidzakuturutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiramo; m'menemo udzafa.
27
Koma kudziko kumene moyo wao ukhumba kubwerera, kumeneko sadzabwerako.
28
Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? cifukwa canji aturutsidwa iye, ndi mbeu zace, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?
29
Iwe dziko, dziko, dziko lapansi, tamvera mau a Yehova.
30
Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ace; pakuti palibe munthu wa mbeu zace adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi kulamuliranso m'Yuda.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52