bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Chronicles 11
1 Chronicles 11
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 12 →
1
Pamenepo Aisraele onse anasonkhana kwa Davide ku Hebroni, ndi kuti, Taonani, ife ndife fupa lanu, ndi mnofu wanu.
2
Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele.
3
Akulu onse omwe a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israele monga mwa mau a Yehova, ndi dzanja la Samuele.
4
Namuka Davide ndi Aisraele onse naye ku Yerusalemu, ndiwo Yebusi; ndipo Ayebusi nzika za m'dziko zinali komweko.
5
Ndipo nzika za m'Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mudzi wa Davide.
6
Nati Davide, Aliyense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yowabu mwana wa Zeruya, nakhala mkulu iyeyu.
7
Ndipo Davide anakhala m'lingamo; chifukwa chake analitcha mudzi wa Davide.
8
Ndipo anamanga mudzi pozungulira pake, kuyambira ku Milo ndi pozungulira pake; ndi Yowabu anakonzanso potsala pa mudzi.
9
Ndipo Davide anakulakulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye.
10
Akulu a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye m'ufumu wake, pamodzi ndi Aisraele onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israele, ndi awa.
11
Kuwerenga kwa amphamvu aja Davide anali nao ndi uku: Yasobeamu mwana wa Muhakimoni, mkulu wa makumi atatu aja, anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha nthawi imodzi.
12
Ndi pambuyo pake Eleazara mwana wa Dodo Mwahohi, ndiye mmodzi wa atatu aja amphamvu.
13
Anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.
14
Koma anadziimika pakati pa munda, naulanditsa, nakantha Afilisti; m'mwemo anawapulumutsa Yehova ndi chipulumutso chachikulu.
15
Ndipo atatu a akulu makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'chigwa cha Refaimu.
16
Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la asilikali a Afilisti linali ku Betelehemu.
17
Ndipo Davide analakalaka, nati, Ha? Mwenzi wina atandimwetsa madzi a m'chitsime cha ku Betelehemu chili kuchipata.
18
Napyola atatuwo misasa ya Afilisti natunga madzi ku chitsime cha ku Betelehemu chili kuchipata, nabwera nao kwa Davide; koma Davide anakana kumwako, koma anawathirira kwa Yehova;
19
nati, Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kuchita ichi. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wao, inde akadataya moyo wao, pakukatenga madziwa. M'mwemo sanafune kuwamwa. Izi anazichita atatu amphamvuwa.
20
Ndipo Abisai mbale wa Yowabu, ndiye wamkulu wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.
21
Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkulu wao; koma sanafike pa atatu oyamba aja.
22
Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabizeeli, wochita zachikulu, anapha ana awiri a Ariyele wa ku Mowabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya chipale chofewa.
23
Anaphanso Mwejipito munthu wamkulu, msinkhu wake mikono isanu, ndi m'dzanja la Mwejipito munali mkondo ngati mtanda woombera nsalu; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wake womwe.
24
Izi anazichita Benaya mwana wa Yehoyada, namveka dzina mwa atatu amphamvuwo.
25
Taonani, anali wa ulemu woposa makumi atatuwo, koma sanafike pa atatu oyamba aja; ndipo Davide anamuika mkulu wa olindirira ake.
26
Ndipo amphamvuwo a magulu a nkhondo ndiwo Asahele mbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
27
Samoti Muharodi, Helezi Mpeloni,
28
Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiyezere wa ku Anatoti,
29
Sibekai Muhusa, Ilai Mwahohi,
30
Maharai Mnetofa, Heledi mwana wa Baana Mnetofa,
31
Itai mwana wa Ribai wa Gibea wa ana a Benjamini, Benaya Mpiratoni,
32
Hurai wa ku mitsinje ya Gaasi, Abiyele Mwarabati,
33
Azimaveti Mbaharumi, Eliyaba Msaaliboni;
34
ana a Hasemu Mgizoni; Yonatani mwana wa Sage Muharari,
35
Ahiyamu mwana wa Sakara Muharari, Elifala mwana wa Uri,
36
Hefere Mmekerati, Ahiya Mpeloni,
37
Heziro wa ku Karimele, Naarai mwana wa Ezibai,
38
Yowele mbale wa Natani, Mibara mwana wa Hagiri,
39
Zeleki Mwamoni, Naharai Mbeeroti wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya,
40
Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri,
41
Uriya Muhiti, Zabadi mwana wa Alai,
42
Adina mwana wa Siza Mrubeni mkulu wa Arubeni, ndi makumi atatu pamodzi naye,
43
Hanani mwana wa Maaka, ndi Yosafati Mmitini,
44
Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyele ana a Hotamu wa ku Aroere,
45
Yediyaele mwana wa Simiri, ndi Yoha mbale wake Mtizi,
46
Eliyele Mmahavi, ndi Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, ndi Itima Mmowabu,
47
Eliyele, ndi Obedi, ndi Yaasiyele Mmezobai.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29