bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Chronicles 24
1 Chronicles 24
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 25 →
1
Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
2
Koma Nadabu ndi Abihu anafa, atate wao akali ndi moyo, opanda ana; momwemo Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe.
3
Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleki wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao m'utumiki wao.
4
Ndipo anapeza kuti amuna akulu a ana a Eleazara anachuluka, a ana a Itamara anachepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akulu a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.
5
Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.
6
Ndi Semaya mwana wa Netanele mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, a akulu a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lake ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.
7
Ndipo maere oyamba anamgwera Yehoyaribu, wachiwiri Yedaya,
8
wachitatu Harimu, wachinai Seorimu,
9
wachisanu Malikiya, wachisanu ndi chimodzi Miyamini,
10
wachisanu ndi chiwiri Hakozi, wachisanu ndi chitatu Abiya,
11
wachisanu ndi chinai Yesuwa, wakhumi Sekaniya,
12
wakhumi ndi chimodzi Eliyasibu, wakhumi ndi chiwiri Yakimu,
13
wakhumi ndi chitatu Hupa, wakhumi ndi chinai Yesebeabu,
14
wakhumi ndi chisanu Biliga, wakhumi ndi chisanu ndi chimodzi Imeri,
15
wakhumi ndi chisanu ndi chiwiri Heziri, wakhumi ndi chisanu ndi chitatu Hapizeze,
16
wakhumi ndi chisanu ndi chinai Petahiya, wa makumi awiri Yehezikele,
17
wa makumi awiri ndi chimodzi Yakini, wa makumi awiri ndi chiwiri Gamuli,
18
wa makumi awiri ndi chitatu Delaya, wa makumi awiri ndi chinai Maaziya.
19
Awa ndi malongosoledwe ao m'utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa chiweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israele anamlamulira.
20
Ndipo wa ana otsala a Levi: wa ana a Amuramu, Subaele; wa ana a Subaele, Yedeiya.
21
Wa Rehabiya: wa ana a Rehabiya, mkulu ndi Isiya.
22
Wa Aizihara: Selomoti; wa ana a Selomoti, Yahati.
23
Ndi wa ana a Hebroni: mkulu ndi Yeriya, wachiwiri Amariya, wachitatu Yahaziele, wachinai Yekameamu.
24
Wa ana a Uziyele, Mika; wa ana a Mika, Samiri.
25
Mbale wa Mika, Isiya; a ana a Isiya, Zekariya.
26
Ana a Merari: Mali ndi Musi; mwana wa Yaziya, Beno.
27
Ana a Merari: wa Yaziya, Beno, ndi Sohamu, ndi Zakuri, ndi Ibiri.
28
Wa Mali: Eleazara, ndiye wopanda ana.
29
Wa Kisi: mwana wa Kisi, Yerameele.
30
Ndi ana a Musi: Mali, ndi Edere, ndi Yerimoti. Awa ndi ana a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.
31
Awanso anachita maere monga abale ao ana a Aroni, pamaso pa Davide mfumu, ndi Zadoki, ndi Ahimeleki, ndi akulu a nyumba za makolo za ansembe ndi Alevi; mkulu wa nyumba za makolo monga mng'ono wake.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29