bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Chronicles 29
1 Chronicles 29
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
1
Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomoni yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo ntchitoyi ndi yaikulu, pakuti chinyumbachi sichili cha munthu, koma cha Yehova Mulungu.
2
Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golide wa zija zagolide ndi siliva wa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, chitsulo cha zija zachitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawangamawanga, ndi miyala ya mtengo wake ya mitundumitundu ndi miyala yansangalabwe yochuluka.
3
Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;
4
ndicho matalente zikwi zitatu za golide, golide wa Ofiri; ndi matalente zikwi zisanu ndi ziwiri a siliva woyengetsa, kumamatiza nazo makoma a nyumbazi;
5
golide wa zija zagolide, ndi siliva wa zija zasiliva, ndi za ntchito zilizonse akuzipanga manja a amisiri. Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira kwa Yehova lero lino?
6
Pamenepo akulu a nyumba za makolo, ndi akulu a mafuko a Israele, ndi akulu a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira ntchito ya mfumu, anapereka mwaufulu,
7
napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golide matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi chitsulo matalente zikwi zana limodzi.
8
Ndipo amene anali nayo miyala ya mtengo wake anaipereka ku chuma cha nyumba ya Yehova, mwa dzanja la Yehiyele Mgeresoni.
9
Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu.
10
Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.
11
Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.
12
Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.
13
Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.
14
Koma ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? Popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.
15
Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.
16
Yehova Mulungu wathu, zounjikika izi zonse tazikonzeratu kukumangirani Inu nyumba ya dzina lanu loyera zifuma ku dzanja lanu, zonsezi ndi zanu.
17
Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.
18
Yehova Mulungu wa Abrahamu, wa Isaki, ndi wa Israele makolo athu, musungitse ichi kosatha m'chilingaliro cha maganizo a mtima wa anthu anu, nimulunjikitse mitima yao kwanu,
19
nimupatse Solomoni mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kuchita izi zonse, ndi kumanga chinyumbachi chimene ndakonzeratu mirimo yake.
20
Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.
21
Ndipo anamphera Yehova nsembe, napereka nsembe zopsereza kwa Yehova m'mawa mwake mwa tsiku lija, ndizo ng'ombe chikwi chimodzi, nkhosa zamphongo chikwi chimodzi, ndi anaankhosa chikwi chimodzi, pamodzi ndi nsembe zao zothira, ndi nsembe zochuluka za Aisraele onse:
22
nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi chimwemwe chachikulu. Ndipo analonga ufumu Solomoni mwana wa Davide kachiwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe.
23
Momwemo Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Yehova, ndiye mfumu m'malo mwa Davide atate wake, nalemerera, namvera iye Aisraele onse.
24
Ndi akulu onse, ndi amuna amphamvu onse, ndi ana amuna onse omwe a mfumu Davide, anagonjeratu kwa Solomoni mfumu.
25
Ndipo Yehova anakuza Solomoni kwakukulu pamaso pa Aisraele onse, nampatsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israele inali nao wotero.
26
Momwemo Davide mwana wa Yese adakhala mfumu ya Aisraele onse.
27
Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israele ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu m'Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu m'Yerusalemu.
28
Nafa atakalamba bwino, wochuluka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
29
Zochita mfumu Davide tsono, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Samuele mlauli, ndi m'buku la mau a Natani mneneri, ndi m'buku la mau a Gadi mlauli;
30
pamodzi ndi za ufumu wake wonse, ndi mphamvu yake, ndi za nthawizo zidampitira iye, ndi Israele, ndi maufumu onse a maiko.
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29