bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Chronicles 6
1 Chronicles 6
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 7 →
1
Ana a Levi: Geresomo, Kohati, ndi Merari.
2
Ndi ana a Kohati: Amuramu, Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele.
3
Ndi ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriyamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
4
Eleazara anabala Finehasi, Finehasi anabala Abisuwa,
5
ndi Abisuwa anabala Buki, ndi Buki anabala Uzi,
6
ndi Uzi anabala Zerahiya, ndi Zerahiya anabala Meraiyoti,
7
Meraiyoti anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubi,
8
ndi Ahitubi anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Ahimaazi,
9
ndi Ahimaazi anabala Azariya, ndi Azariya anabala Yohanani,
10
ndi Yohanani anabala Azariya (ndiye amene anachita ntchito ya nsembe m'nyumba anaimanga Solomoni m'Yerusalemu),
11
ndi Azariya anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubi,
12
ndi Ahitubi anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Salumu,
13
ndi Salumu anabala Hilikiya, ndi Hilikiya anabala Azariya,
14
ndi Azariya anabala Seraya, ndi Seraya anabala Yehozadaki,
15
ndi Yehozadaki analowa undende muja Yehova anatenga ndende Yuda ndi Yerusalemu ndi dzanja la Nebukadinezara.
16
Ana a Levi: Geresomo, Kohati ndi Merari.
17
Ndipo maina a ana a Geresomo ndi awa: Libini, ndi Simei.
18
Ndipo ana a Kohati ndiwo Amuramu, ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele.
19
Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao ndi awa.
20
Wa Geresomo: Libini mwana wake, Yahati mwana wake, Zima mwana wake,
21
Yowa mwana wake, Ido mwana wake, Zera mwana wake, Yeterai mwana wake.
22
Ana a Kohati: Aminadabu mwana wake, Kora mwana wake, Asiri mwana wake,
23
Elikana mwana wake, ndi Ebiyasafu mwana wake, ndi Asiri mwana wake,
24
Tahati mwana wake, Uriyele mwana wake, Uziya mwana wake, ndi Shaulo mwana wake.
25
Ndi ana a Elikana: Amasai, ndi Ahimoti.
26
Elikana: ana a Elikana Zofai mwana wake, ndi Nahati mwana wake,
27
Eliyabu mwana wake, Yerohamu mwana wake, Elikana mwana wake.
28
Ndi ana a Samuele: woyamba Yowele, ndi wachiwiri Abiya.
29
Ana a Merari: Mali, Libini mwana wake, Simei mwana wake, Uza mwana wake,
30
Simea mwana wake, Hagiya mwana wake, Asaya mwana wake.
31
Ndipo iwo aja Davide anawaimika a udindo wa nyimbo m'nyumba ya Yehova, litafikira kupumula likasalo, ndi awa.
32
Ndipo anatumikira ndi kuimba pakhomo pa Kachisi wa chihema chokomanako mpaka Solomoni adamanga nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, naimirira m'utumiki wao monga mwa malongosoledwe ao.
33
Ndipo oimirirawo, ndi ana ao, ndi awa: a ana a Akohati, Hemani woimbayo, mwana wa Yowele, mwana wa Samuele,
34
mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Eliyele, mwana wa Towa,
35
mwana wa Zufu, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,
36
mwana wa Elikana, mwana wa Yowele, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,
37
mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,
38
mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, mwana wa Israele.
39
Ndi mbale wake Asafu wokhala ku dzanja lake lamanja, ndiye Asafu mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,
40
mwana wa Mikaele, mwana wa Baaseiya, mwana wa Malikiya,
41
mwana wa Etini, mwana wa Zera, mwana wa Adaya,
42
mwana wa Etani, mwana wa Zima, mwana wa Simei,
43
mwana wa Yahati, mwana wa Geresomo, mwana wa Levi.
44
Ndi ku dzanja lamanzere abale ao ana a Merari: Etani mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki,
45
mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,
46
mwana wa Amizi, mwana wa Bani, mwana wa Semeri,
47
mwana wa Mali, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi.
48
Ndi abale ao Alevi anaikidwa achite za utumiki zilizonse za Kachisi wa nyumba ya Mulungu.
49
Koma Aroni ndi ana ake ankafukiza pa guwa la nsembe yopsereza, ndi pa guwa la nsembe yofukiza, chifukwa cha ntchito yonse ya malo opatulika kwambiri, ndi kuchitira Israele chowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.
50
Ndipo ana a Aroni ndiwo Eleazara mwana wake, Finehasi mwana wake, Abisuwa mwana wake,
51
Buki mwana wake, Uzi mwana wake, Zerahiya mwana wake,
52
Meraiyoti mwana wake, Amariya mwana wake, Ahitubi mwana wake,
53
Zadoki mwana wake, Ahimaazi mwana wake.
54
Pokhala pao tsono monga mwa madera ao m'malire mwao ndi awa: kwa ana a Aroni a mabanja a Akohati, pakuti maere oyamba adagwera iwowa,
55
kwa iwo anapereka Hebroni m'dziko la Yuda, ndi podyetsa pake pozungulira pake;
56
koma minda ya mudzi ndi milaga yake anapatsa Kalebe mwana wa Yefune.
57
Ndi kwa ana a Aroni anapereka midzi yopulumukirako: Hebroni, ndi Libina ndi mabusa ake, ndi Yatiri, ndi Esitemowa ndi mabusa ake.
58
Ndi Hileni ndi mabusa ake, ndi Debiri ndi mabusa ake,
59
ndi Asani ndi mabusa ake, ndi Betesemesi ndi mabusa ake;
60
ndi ku fuko la Benjamini Geba ndi mabusa ake, ndi Alemeti ndi mabusa ake, ndi Anatoti ndi mabusa ake. Midzi yao yonse mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu.
61
Ndipo otsala a ana a Kohati analandira mwa maere, motapa pa mabanja a fuko, pa fuko la Manase logawika pakati, midzi khumi.
62
Ndi kwa ana a Geresomo monga mwa mabanja ao, motapa pa fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa fuko la Manase m'Basani, midzi khumi ndi itatu.
63
Ana a Merari analandira mwa maere monga mwa mabanja ao, motapa pa fuko la Rubeni, ndi pa fuko la Gadi, ndi pa fuko la Zebuloni, midzi khumi ndi iwiri.
64
Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi midzi ndi mabusa ao.
65
Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la ana a Benjamini, midzi iyi yotchulidwa maina ao.
66
Ndi mabanja ena a ana a Kohati anali nayo midzi ya malire ao, yotapa pa fuko la Efuremu.
67
Ndipo anawapatsa midzi yopulumukiramo: Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, Gezere ndi mabusa ake,
68
ndi Yokomeamu ndi mabusa ake, ndi Betehoroni ndi mabusa ake,
69
ndi Ayaloni ndi mabusa ake, ndi Gatirimoni ndi mabusa ake,
70
ndi motapa pa fuko la Manase logawika pakati, Anere ndi mabusa ake, ndi Bileamu ndi mabusa ake, kwa otsala a mabanja a ana a Kohati.
71
Ana a Geresomo analandira motapa pa mabanja a fuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basani ndi mabusa ake, ndi Asitaroti ndi mabusa ake;
72
ndi motapa pa fuko la Isakara, Kedesi ndi mabusa ake, Daberati ndi mabusa ake,
73
ndi Ramoti ndi mabusa ake, ndi Anemu ndi mabusa ake;
74
ndi motapa pa fuko la Asere, Masala ndi mabusa ake, ndi Abidoni ndi mabusa ake,
75
ndi Hukoki ndi mabusa ake, ndi Rehobu ndi mabusa ake;
76
ndi motapa pa fuko la Nafutali, Kedesi m'Galileya ndi mabusa ake, ndi Hamoni ndi mabusa ake, ndi Kiriyataimu ndi mabusa ake.
77
Amerari (otsala a Alevi) analandira, motapa pa fuko la Zebuloni, Rimoni ndi mabusa ake, Tabori ndi mabusa ake;
78
ndi tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko analandira, motapa pa fuko la Rubeni, Bezeri m'chipululu ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake,
79
ndi Kedemoti ndi mabusa ake, ndi Mefaati ndi mabusa ake;
80
ndi motapa m'fuko la Gadi, Ramoti m'Giliyadi ndi mabusa ake, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake,
81
ndi Hesiboni ndi mabusa ake, ndi Yazere ndi mabusa ake.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29