bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Chronicles 14
1 Chronicles 14
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 15 →
1
Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide, ndi mikungudza, ndi amisiri omanga miyala, ndi amatabwa, kuti ammangire nyumba.
2
Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova adamkhazikitsa mfumu ya Israele; pakuti ufumu wake unakwezekadi, chifukwa cha anthu ake Israele.
3
Ndipo Davide anatenga akazi ena ku Yerusalemu, nabala Davide ana aamuna ndi aakazi ena.
4
Maina a ana anali nao m'Yerusalemu ndi awa: Samuwa, ndi Sobabu Natani, ndi Solomoni,
5
ndi Ibara, ndi Elisuwa, ndi Elipeleti,
6
ndi Noga, ndi Nefegi, ndi Yafiya,
7
ndi Elisama, ndi Beeliyada, ndi Elifeleti.
8
Pamene Afilisti anamva kuti anamdzoza Davide akhale mfumu ya Aisraele onse, Afilisti onse anakwera kufunafuna Davide; ndipo Davide anamva, nawatulukira.
9
Afilisti tsono anafika, nafalikira m'chigwa cha Refaimu.
10
Ndipo Davide anafunsira kwa Mulungu, kuti, Ndikwere kodi kuyambana ndi Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova anati kwa iye, Kwera, pakuti ndidzawapereka m'dzanja lako.
11
Atafika tsono ku Baala-Perazimu, Davide anawakantha komweko; nati Davide, Mulungu anapasula adani anga ndi dzanja langa, ngati pokhamulira madzi. Chifukwa chake analitcha dzina la malowo Baala-Perazimu.
12
Ndipo anasiyako milungu yao; nalamula Davide, ndipo anaitentha ndi moto.
13
Ndipo Afilisti anabwerezanso, nafalikira m'chigwamo.
14
Ndipo Davide anafunsiranso kwa Mulungu, nanena Mulungu naye, Usakwera kuwatsata, uwazungulire, nuwadzere pandunji pa mitengo ya mkandankhuku.
15
Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula kunsonga kwa mitengo ya mkandankhuku, pamenepo utulukire kunkhondo; pakuti Mulungu watulukira pamaso pako kukantha gulu la Afilisti.
16
Nachita Davide monga Yehova adamuuza, nakantha gulu la Afilisti kuyambira ku Gibiyoni kufikira ku Gezere.
17
Ndipo mbiri ya Davide inabuka m'maiko onse, nafikitsira Yehova kuopsa kwake pa amitundu onse.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29