bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Chronicles 27
1 Chronicles 27
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 28 →
1
Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.
2
Woyang'anira chigawo choyamba cha mwezi, woyamba ndiye Yasobeamu mwana wa Zabidiele; m'chigawo mwake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
3
Ndiye wa ana a Perezi, mkulu wa akazembe onse a khamu mwezi woyamba.
4
Woyang'anira chigawo cha mwezi wachiwiri ndiye Dodai Mwahohi ndi chigawo chake; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m'chigawo chake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
5
Kazembe wachitatu wa khamu wa mwezi wachitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkulu; ndi m'chigawo mwake munalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai.
6
Benaya ameneyo ndiye wamphamvu uja wa makumi atatu aja, woyang'anira chigawo chake ndi Amizabadi mwana wake.
7
Wachinai wa mwezi wachinai ndiye Asahele mbale wa Yowabu, ndi pambuyo pake Zebadiya mwana wake; ndi m'chigawo mwake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
8
Kazembe wachisanu wa mwezi wachisanu ndiye Samuti Mwizara; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
9
Wachisanu ndi chimodzi wa mwezi wachisanu ndi chimodzi ndiye Ira mwana wa Ikesi Mtekowa; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
10
Wachisanu ndi chiwiri wa mwezi wachisanu ndi chiwiri ndiye Helezi Mpeloni wa ana a Efuremu; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
11
Wachisanu ndi chitatu wa mwezi wachisanu ndi chitatu ndiye Sibekai Muhusa wa Azera; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
12
Wachisanu ndi chinai wa mwezi wachisanu ndi chinai ndiye Abiyezere Mwanatoti wa Abenjamini; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
13
Wakhumi wa mwezi wakhumi ndiye Maharai Mnetofa wa Azera; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
14
Wakhumi ndi chimodzi wa mwezi wakhumi ndi chimodzi ndiye Benaya Mpiratoni wa ana a Efuremu; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
15
Wakhumi ndi chiwiri wa mwezi wakhumi ndi chiwiri ndiye Helidai Mnetofa wa Otiniyele; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
16
Koma oyang'anira mafuko a Israele ndi awa: wa Arubeni mtsogoleri wao ndiye Eliyezere mwana wa Zikiri; wa Asimeoni, Sefatiya mwana wa Maaka;
17
wa Alevi, Hasabiya mwana wa Kemuwele; wa Aroni, Zadoki;
18
wa Yuda, Elihu mbale wina wa Davide; wa Isakara, Omuri mwana wa Mikaele;
19
wa Zebuloni, Isimaya mwana wa Obadiya; wa Nafutali, Yerimoti mwana wa Aziriele;
20
wa ana a Efuremu, Hoseya mwana wa Azaziya; wa fuko la Manase logawika pakati, Yowele mwana wa Pedaya;
21
wa fuko la Manase logawika pakati m'Giliyadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yaasiyele mwana wa Abinere;
22
wa Dani, Azarele mwana wa Yerohamu. Awa ndi akazembe a mafuko a Israele.
23
Koma Davide sanawerenge iwo a zaka makumi awiri ndi ochepapo, pakuti Yehova adati kuti adzachulukitsa Israele ngati nyenyezi za kuthambo.
24
Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsirize; ndi mkwiyo unagwera Israele chifukwa cha ichi, ndipo chiwerengo chao sichinalembedwa m'buku la mbiri ya mfumu Davide.
25
Ndipo woyang'anira chuma cha mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyele, ndi woyang'anira wa chuma cha m'minda, m'mizinda ndi m'milaga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;
26
ndi woyang'anira iwo akugwira ntchito ya m'munda yakulima nthaka ndiye Eziri mwana wa Kelubu;
27
ndi woyang'anira minda yamphesa ndiye Simei Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yamphesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifamu;
28
ndi woyang'anira mitengo ya azitona, ndi yamikuyu yokhala kuzidikha kunsi, ndiye Baala-Hanani Mgederi; ndi woyang'anira zosungiramo mafuta ndiye Yowasi;
29
ndi woyang'anira ng'ombe zakudya m'Saroni ndiye Sitirai Msaroni; ndi woyang'anira ng'ombe za m'zigwa ndiye Safati mwana wa Adilai;
30
ndi woyang'anira ngamira ndiye Obili Mwismaele; ndi woyang'anira abulu ndiye Yedeiya Mmeronoti;
31
ndi woyang'anira zoweta zazing'ono ndiye Yazizi Mhagiri. Onsewa ndiwo akulu a zolemera zake za mfumu Davide.
32
Ndipo Yonatani atate wake wina wa Davide anali phungu, munthu wanzeru ndi mlembi; ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni anakhala ndi ana a mfumu;
33
ndi Ahitofele anali phungu wa mfumu, ndi Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu;
34
ndi wotsatana ndi Ahitofele, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abiyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yowabu.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29