bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Chronicles 17
1 Chronicles 17
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 18 →
1
Ndipo pokhala Davide m'nyumba mwake, Davideyo anati kwa Natani mneneri, Taona, ndikhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la chipangano la Yehova likhala m'nsalu zotchinga.
2
Ndipo Natani anati kwa Davide, Muchite zonse zili m'mtima mwanu; pakuti Mulungu ali nanu.
3
Ndipo usiku womwewo mau a Mulungu anadzera Natani, ndi kuti,
4
Kauze Davide mtumiki wanga, Atero Yehova, Usandimangire nyumba yokhalamo;
5
pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinakwera naye Israele, kufikira lero lino; koma ndakhala ndikuyenda m'mahema uku ndi uku.
6
Pali ponse ndinayenda nao Aisraele onse ndinanena kodi mau ndi woweruza aliyense wa Israele, amene ndinamuuza adyetse anthu anga, ndi kuti, Mwalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?
7
Chifukwa chake tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Ambuye wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele;
8
ndipo ndakhala ndi iwe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akulu okhala padziko.
9
Ndipo ndaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;
10
ndi kuyambira kuja ndinaika oweruza ayang'anire anthu anga Israele; ndipo ndagonjetsa adani ako onse. Ndikuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.
11
Ndipo kudzachitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.
12
Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wake kosatha.
13
Ndidzakhala atate wake, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamchotsera chifundo changa monga muja ndinachotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;
14
koma ndidzamkhazikitsa m'nyumba mwanga, ndi m'ufumu wanga kosatha; ndi mpando wa chifumu wake udzakhazikika kosatha.
15
Monga mwa mau awa onse, ndi monga mwa masomphenya awa onse, momwemo Natani analankhula ndi Davide.
16
Pamenepo mfumu Davide analowa nakhala pamaso pa Yehova, nati, Ndine yani, Yehova Mulungu, ndi nyumba yanga njotani kuti mwandifikitsa mpaka pano?
17
Ndipo ichi nchaching'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.
18
Anenenjinso Davide kwa inu za ulemu wochitikira mtumiki wanu? Pakuti mudziwa mtumiki wanu.
19
Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwachita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikulu izi zonse.
20
Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu.
21
Ndiwo ayani akunga anthu anu Israele, mtundu wa pa wokha wa pa dziko lapansi, amene Mulungu anakadziombolera mtundu wa anthu, kudzibukitsira dzina, mwa zazikulu ndi zoopsa, pakupirikitsa amitundu pamaso pa anthu anu amene munawaombola m'Ejipito?
22
Pakuti anthu anu Israele mudawayesa anthu anuanu kosatha; ndipo Inu, Yehova, munayamba kukhala Mulungu wao.
23
Ndipo tsopano, Yehova, akhazikike kosalekeza mau mudanenawa za mtumiki wanu, ndi za nyumba yake, nimuchite monga mwanena.
24
Inde likhazikike dzina lanu, likulitsidwe kosalekeza, ndi kuti, Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele; akhalira Israele Mulungu; ndi nyumba ya Davide mtumiki wanu ikhazikika pamaso panu.
25
Pakuti Inu, Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzammangira banja; momwemo mtumiki wanu waona mtima wakupemphera pamaso panu.
26
Ndipo tsopano, Yehova, Inu ndinu Mulungu, ndipo mwanenera mtumiki wanu chokoma ichi;
27
chakukomerani kudalitsa nyumba ya mtumiki wanu, kuti ikhalebe kosatha pamaso panu; pakuti Inu Yehova mwadalitsa, ndipo idzadalitsika kosatha.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29