bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jeremiah 13
Jeremiah 13
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 14 →
1
Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'chuuno mwako, usauike m'madzi.
2
Ndipo ndinagula mpango monga mwa mau a Yehova, ndi kuvala m'chuuno mwanga.
3
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti,
4
Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'chuuno mwako, nuuke, nupite ku Yufurate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala.
5
Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Yufurate, monga Yehova anandiuza ine.
6
Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati mwa ine, Uka, pita ku Yufurate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.
7
Ndipo ndinanka ku Yufurate, ndikumba, nditenga mpango m'malo m'mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu.
8
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,
9
Yehova atero, Momwemo ndidzaononga kudzitama kwa Yuda, ndi kudzitama kwakukulu kwa Yerusalemu.
10
Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.
11
Pakuti monga mpango uthina m'chuuno cha munthu, chomwecho ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israele ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi chilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.
12
Chifukwa chake uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo?
13
Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi chiledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala m'Yerusalemu.
14
Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi chisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi chifundo, chakuti ndisawaononge.
15
Tamvani inu, Tcherani khutu; musanyade, pakuti Yehova wanena.
16
Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanakhumudwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.
17
Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.
18
Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.
19
Midzi ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda wonse wachotsedwa m'ndende wonsewo, wachotsedwa m'nsinga.
20
Tukulani maso anu, taonani iwo amene achokera kumpoto; zili kuti zoweta zinapatsidwa kwa iwe, zoweta zako zokoma?
21
Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?
22
Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zithende zako zaphwetekwa.
23
Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa.
24
Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu.
25
Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.
26
Chifukwa chake Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka.
27
Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52