bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jeremiah 48
Jeremiah 48
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 49 →
1
Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.
2
Palibenso kutamanda Mowabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.
3
Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu!
4
Mowabu waonongedwa; ang'ono ake amveketsa kulira.
5
Pakuti adzakwera pa chikweza cha Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa chitsiko cha Horonaimu amva kulira kowawa kwa chionongeko.
6
Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amaliseche m'chipululu.
7
Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.
8
Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uliwonse; chigwa chomwe chidzasakazidwa, ndipo chidikha chidzaonongedwa; monga wanena Yehova.
9
Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; midzi yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.
10
Atembereredwe iye amene agwira ntchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lake kumwazi.
11
Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthika.
12
Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao.
13
Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira.
14
Muti bwanji, Tili amphamvu, olimba mtima ankhondo?
15
Mowabu wapasuka, akwera kulowa m'midzi yake, ndi anyamata ake osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lake ndiye Yehova wa makamu.
16
Tsoka la Mowabu layandikira kudza, nsautso yake ifulumiratu.
17
Inu nonse akumzungulira, mumchitire iye chisoni, inu nonse akudziwa dzina lake; muti, Chibonga cholimba chathyokatu, ndodo yokoma!
18
Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.
19
Iwe wokhala m'Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani?
20
Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.
21
Chiweruzo chafika pa dziko lachidikha; pa Holoni, ndi pa Yahazi, ndi pa Mefaati;
22
ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Betedibilataimu;
23
ndi pa Kiriyataimu, ndi pa Betegamuli, ndi pa Betemeoni;
24
ndi pa Keriyoti, ndi pa Bozira, ndi pa midzi yonse ya dziko la Mowabu, yakutali kapena yakufupi.
25
Nyanga ya Mowabu yaduka, ndipo wathyoka mkono wake, ati Yehova.
26
Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Mowabu yemwe adzavimvinika m'kusanza kwake, ndipo iye adzasekedwanso.
27
Kodi sunaseka Israele? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? Pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.
28
Inu okhala m'Mowabu, siyani midzi, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje.
29
Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake.
30
Ine ndidziwa mkwiyo wake, ati Yehova, kuti uli chabe; zonyenga zake sizinachita kanthu.
31
Chifukwa chake ndidzakuwira Mowabu; inde, ndidzafuulira Mowabu yense, adzalirira anthu a ku Kiriheresi.
32
Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako.
33
Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula.
34
Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa madzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.
35
Ndiponso ndidzaletsa m'Mowabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yake.
36
Chifukwa chake mtima wanga umlirira Mowabu monga zitoliro, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kiriheresi monga zitoliro, chifukwa chake zakuchuluka zake adadzionera zatayika.
37
Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zosengedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli.
38
Pamwamba pa machindwi a Mowabu ndi m'miseu mwake muli kulira monsemonse; pakuti ndaswa Mowabu monga mbiya m'mene mulibe chikondwero, ati Yehova.
39
Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye.
40
Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati chiombankhanga, adzamtambasulira Mowabu mapiko ake.
41
Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.
42
Ndipo Mowabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, chifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.
43
Mantha, ndi dzenje, ndi khwekhwe, zili pa iwe, wokhala m'Mowabu, ati Yehova.
44
Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.
45
Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka m'Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamtu pa ana a phokoso.
46
Tsoka iwe, Mowabu! Anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako amuna atengedwa ndende, ndi ana ako akazi atengedwa ndende.
47
Koma ndidzabwezanso undende wa Mowabu masiku akumaliza, ati Yehova. Ziweruzo za Mowabu ndi zomwezi.
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 49 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52