bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jeremiah 41
Jeremiah 41
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 42 →
1
Ndipo panali mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkulu wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi m'Mizipa.
2
Ndipo anauka Ismaele mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babiloni inamuika wolamulira dziko.
3
Ismaele naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Ababiloni amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo.
4
Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa,
5
anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makamu asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.
6
Ndipo Ismaele mwana wa Netaniya anatuluka m'Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wake wa Ahikamu.
7
Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mudzi, Ismaele mwana wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye.
8
Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismaele, Musatiphe ife; pakuti tili ndi chuma chobisika m'mudzi, cha tirigu, ndi cha barele, ndi cha mafuta, ndi cha uchi. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.
9
Ndipo dzenje moponyamo Ismaele mitembo yonse ya anthu amene anawapha, chifukwa cha Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa chifukwa cha kuopa Baasa mfumu ya Israele, lomwelo Ismaele mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.
10
Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala m'Mizipa, ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala m'Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.
11
Koma pamene Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo akhala naye, anamva zoipa zonse anazichita Ismaele mwana wa Netaniya,
12
anatenga anthu onse, nanka kukamenyena ndi Ismaele mwana wa Netaniya, nampeza pa madzi ambiri a m'Gibiyoni.
13
Ndipo panali pamene anthu onse amene anali ndi Ismaele anaona Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, anasekera.
14
Ndipo anthu onse amene Ismaele anatenga ndende kuwachotsa m'Mizipa anatembenuka nabwera, nanka kwa Yohanani mwana wake wa Kareya.
15
Koma Ismaele mwana wake wa Netaniya anapulumuka Yohanani ndi anthu asanu ndi atatu, nanka kwa ana a Amoni.
16
Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismaele mwana wake wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibiyoni;
17
ndipo anachoka, natsotsa m'Geruti-Kimuhamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa m'Ejipito,
18
chifukwa cha Ababiloni; pakuti anawaopa, chifukwa Ismaele mwana wake wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni anamuika wolamulira m'dzikomo.
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 42 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52