bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jeremiah 46
Jeremiah 46
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 47 →
1
Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri akunena za amitundu.
2
Za Ejipito: kunena za nkhondo ya Farao Neko mfumu ya Aejipito, imene inali pa mtsinje wa Yufurate m'Karikemisi, imene anaikantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda.
3
Konzani chikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo.
4
Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.
5
Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.
6
Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pa mtsinje wa Yufurate waphunthwa nagwa.
7
Ndani uyu amene auka ngati Nailo, madzi ake ogavira monga nyanja?
8
Ejipito auka ngati Nailo, madzi ake agavira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ake.
9
Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.
10
Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza chilango, kuti abwezere chilango adani ake; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa mtsinje wa Yufurate.
11
Kwera ku Giliyadi, tenga vunguti, namwali iwe mwana wa Ejipito; wachulukitsa mankhwala chabe; palibe kuchira kwako.
12
Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kufuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.
13
Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adzafika adzakantha dziko la Ejipito.
14
Nenani m'Ejipito, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.
15
Akulimba ako akokoledwa bwanji? Sanaime, chifukwa Yehova anawathamangitsa.
16
Anaphunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzake, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, kudziko la kubadwa kwathu, kuchokera kulupanga lovutitsa.
17
Ndipo anafuula kumeneko, Farao mfumu ya Aejipito ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira.
18
Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika.
19
Mwana wamkazi iwe wokhala m'Ejipito, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsa, mulibenso wokhalamo.
20
Ejipito ndi ng'ombe yaikazi yosalala; chionongeko chituluka kumpoto chafika, chafika.
21
Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.
22
Mkokomo wake udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo.
23
Adzatema nkhalango yake, ati Yehova, pokhala yosapitika; pakuti achuluka koposa dzombe, ali osawerengeka.
24
Mwana wake wamkazi wa Ejipito adzachitidwa manyazi, adzaperekedwa m'manja a anthu a kumpoto.
25
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, ati: Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Ejipito, pamodzi ndi milungu yake, ndi mafumu ake; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;
26
ndipo ndidzawapereka m'manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'manja a atumiki ake; pambuyo pake adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova.
27
Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, iwe Israele: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kuchokera kutali, ndi mbeu yako kudziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m'mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye.
28
Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 47 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52